Kodi Ndiuthenga Uti Womwe Akuwumva?
KODI mungakonde kukhala ndi moyo m’dziko lamtundu wotani? Kodi ana anu mukufuna kuti akhale ndi mtsogolo motani? Ngati kukadakhala kotheka kukhala ndi umoyo wangwiro ndipo osafa konse, kodi mukanausankha?
Kodi mungaŵayankhe motani mafunso amenewo? Anthu ambiri, mosasamala kanthu za chiyambi chawo cha chipembedzo kapena ndale zadziko, amafuna kukhala ndi moyo m’dziko lamtendere ndi la mwana alirenji. Iwo angavomereze dziko lokhala ndi chilungamo changwiro ndi chigwirizano, mmene simukakhala kupereka chiphuphu; mosakhalanso lamulo lina kwa amwaŵi ndi linanso kwa amphaŵi.
Ndipo kwa ana anu, mosakaikira inu mungakonde kukhala ndi zakudya zamwana alirenji, nyumba yabwino, ndi maphunziro abwino. Kufotokoza m’mawu ena, inu mungafune kutsimikizira mtsogolo mwabata kwa inu ndi mbadwa zanu. Ndipo mutapatsidwa mwaŵi, inu mungasankhe kukhala ndi umoyo wangwiro ndi kukhala ndi moyo kwautali woti mukwaniritse zikhumbo zanu zonse zabwino, ngakhale kusangalala ndi moyo wosatha m’dziko lapansi laparadaiso, lamtendere.
Zonsezi sindizo loto losatheka. Ndiwo uthenga wa m’Baibulo umene Mboni za Yehova zikulalikira padziko lonse lapansi, kuphatikizapo m’maiko a Kum’mawa kwa Yuropu.
Chiyembekezo Chopindulitsa cha Baibulo cha Mtsogolo
Maulosi a Baibulo odalirika olembedwa zaka mazana ambiri zapitazo ananeneratu zochitika za m’zaka zathu za zana la 20, ‘nkhondo zathu ndi mbiri zankhondo’; ‘zivomezi zathu ndi kuperewera kwa zakudya mmalo akuti akuti’; ‘kukomoka kwa anthu ndi mantha, ndi kuyembekezera zinthu zirinkudza ku dziko lapansi’; ‘kuwononga kwathu ndikuipitsa dziko lapansi.’—Luka 21:10-33; Chibvumbulutso 11:18.
Komabe, zochitika zonsezi ndi zina zambiri ndizo chizindikiro chotsimikizira chakuti dziko latsopano lolonjezedwa ndi Mulungu lirinso pafupi kwambiri. Ichi chikuphatikizapo “miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano,” ndiko kuti, ulamuliro wa dziko watsopano, boma lakumwamba, ndi chitaganya chapadziko lapansi chosinthidwa momwe ‘mudzakhala chilungamo.’ Chikutanthauza dziko latsopano mmene ‘kuŵaŵa, imfa, ndi maliro sizidzakhalako.’—Yesaya 65:17-25; 2 Petro 3:13; Chibvumbulutso 21:1-4.
Ndithudi, palibe dongosolo landale zadziko, mosasamala kanthu kuti ndilowona mtima chotani kapena losapotoza chotani, lomwe liri lokhoza kukwaniritsa programu yoteroyo. Mfumu Ambuye wachilengedwe chonse yekha, Yehova Mulungu, ndiye ali ndi zonse ziŵiri kufunitsitsa ndi mphamvu za kukwaniritsira ichi. Chinali kaamba ka chifukwa chimenecho chimene Mwana wake, Kristu Yesu, anaphunzitsa atsatiri ake kupemphera kuti: ‘Atate wathu wa kumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.’—Mateyu 6:9, 10.
Kufuna kwa Mulungu nkwakuti dziko lapansi likhale mwala wamtengo wapatali wonyezimira m’chilengedwe chonse, lokhalidwa ndi banja la anthu okonda mtendere. Posachedwapa Mulungu adzachitapo kanthu kuti ichi chichitike. Kadzakhala kachitidwe koyeretsa kuchotsera dziko lapansi zoipitsa zonse ndi oipitsa onse. Kuipitsa konse, kaya kwakuthupi kapena kwamakhalidwe, kudzachotsedweratu padziko lapansi. Kodi adzatsalapo ndani? Yesu anati: ‘Odala ali akufatsa; chifukwa adzalandira dziko lapansi.’—Mateyu 5:5; Chibvumbulutso 16:14-16.
Kodi mukufuna kukhala pakati pa ofatsa omwe adzakhala ndi dalitso la Mulungu? Pamenepo fikirani Mboni za Yehova zokhala pafupi nanu ndikuzipempha phunziro la Baibulo la panyumba laulere, popanda kukulipiritsani mangawa aliwonse. Dzitsimikizireni nokha chimene chiri ‘chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.’ Ndipo kenaka chichiteni.—Aroma 12:2.