Chochitika Chimene Simuyenera Kuphonya
‘Chitani ichi chikumbukiro changa.’ Mawu ameneŵa a Ambuye wathu Yesu Kristu, opezeka pa Luka 22:19, ananenedwa panthaŵi imene iye anakhazikitsa chikumbutso cha imfa yake. Imfa ya Yesu ndiyo inatsegulira anthu chiyembekezo chakupeza moyo wosatha m’mikhalidwe ya Paradaiso. Chotero imfa yake ndichinthu chimene tiyenera kukumbukira. Kodi mudzachita chikumbutso chake chaka chino?
Chonde landirani chiitanochi chochokera kwa Mboni za Yehova chakuti mugwirizane nawo m’kukumbukira chochitika chofunika kwambiri chimenechi. Chikumbukiro chimenechi chidzachitika dzuŵa litaloŵa padeti lolingana ndi Nisani 14 ya kalenda ya Baibulo yozikidwa pa mayendedwe a mwezi. Ikani chizindikiro pa detilo pakalenda yanu kuti musaiŵale. Ilo ndi Loŵeruka, March 30, 1991. Yemwe akukupatsani chiitanochi angakuuzeni malo okumanirako enieniwo ndi nthaŵi.