Uthenga wa Lerolino
Nsanja ya Olonda iri ndi uthenga wotero, monga momwe ananenera woŵerenga wina yemwe posachedwapa anapempha sabusikripishoni. Mkaziyo analemba kuti: “Ndakhala ndikuwêrenga magazini anu ndichikondwerero chachikulu. Ndinali ndi mwaŵi woŵerenga male-mba m’nkhani zosiyanasiyana mkati mwa nthaŵi yanga yopuma.
“Ndimazizwa nthaŵi zonse ndi uthenga wa magazini anu ponena za nyuzi zamakono. Palibe kugogomezera kumene kungachitidwe kosonyeza kufunika kwa mabuku anu kaamba ka kumvetsetsa kwabwinopo kwa Baibulo. Magazini anu ndiwo anandichititsa kutenga Baibulo lodzala ndi fumbi ndi kufufuza m’Bukhulo loposa mabuku onse. Ndimayembekezera mwachidwi kope lirilonse.”
Kodi mungakonde kuti Nsanja ya Olonda itumizidwe kunyumba kwanu? Ngati nditero, chonde dzazani ndi kutumiza kapepala kotsatiraka.