Tsamba 2
Mliri wa Lotale—Kodi Ndani Amapambana? Kodi Ndani Amalephera? 3-9
Mliri wa lotale umayambukira anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse. Ziyembekezo zawo ndi zinyengo zimalenjekeka pa kusankhidwa kokhazikika kwa manambala. Kodi pali mwaŵi wotani wakupambana? Kodi ndani kwenikweni amene amapambana? Kodi ndani amalephera?
Mpira Wachitanyu Wolimbirana Chikho Chapadziko Lonse—Maseŵera Kapena Nkhondo? 10
Mpira wachitanyu ndiwo maseŵera otchuka koposa padziko lonse. Mpikisano wolimbirana Chikho Chapadziko Lonse m’Italiya unagogomezeranso ziyambukiro za utundu ndi mzimu wakupikisana wauchiŵanda. Kodi nkani komwe kali kawonedwe kachikatikati ka maseŵera onse?