Siliri la Ana Okha
Mkazi wina wa ku Fort Worth, Texas, akulemba kuti: “Ndakhala ndi bukhu la Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo kwa zaka zingapo. Ndinasankha kuyamba kuliŵerengera mwana wanga wamwamuna wa miyezi khumi yakubadwa. Tsiku lirilonse ndimaŵerenga mitu iŵiri kapena itatu. Ndidziŵa kuti iye ngwamng’ono kwambiri wosakhoza kulimvetsetsa. Komabe, ndapindula nalo kwakukulu inemwini. Bukhulo linakhudza mtima wanga m’njira yapadera kwambiri ndipo linazamitsa chikondi changa ndi chiyamikiro kwa Yehova Mulungu ndi Mwana wake, Yesu Kristu. Ndiri ndi zaka 27 zakubadwa. Ndinkalingalira kuti bukhu la Mphunzitsi Wamkuru’yo linali la ana okha, ndipo tsopano ndikumva chisoni chifukwa chosaliŵerenga poyambirira.”
Dzazani ndikutumiza kapepala kotsatiraka, ndipo bukhu lachikuto cholimba limeneli, lokhala ndi zithunzithunzi lamasamba 192 lidzatumizidwa kwa inu.
Ndingakonde kulandira bukhu lamasamba 192 la Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo (Kunja kwa Zambia, lemberani nthambi ya Watch Tower yakwanuko kaamba ka chidziŵitso. Onani tsamba 5.)