Tsamba 2
Kodi Muyenera Kusintha Amene Muli? 3-10
Kodi ndinu wogwiritsidwa mwala ndi khalidwe la anthu mwachisawawa? Kodi ndinu wogwiritsidwa mwala ndi khalidwe lanu ndi umunthu wanu? Kodi munakwiitsidwa pamene munayesayesa kumvetsetsa chifukwa chake muli munthu amene muli? Kodi mungasinthe khalidwe lanu? Kodi mungasinthe amene muli?
Kudzichinjiriza—Kodi Mkristu Ayenera Kufika Pati? 12
Kodi Mkristu ayenera kuphunzira ndi kuyeseza judo, kendo, ndi karate? Kodi ndiliti pamene kudzichinjiriza kumakhala koyenera kwa Mkristu?
Zikumbukiro—Mwakungosinika Batani! 23
Anthu ambiri lerolino ali ndi kamera. Koma kodi pali kusiyana kotani pakati pa kujambula ndi kupanga chithunzithunzi? Kodi ndimotani mmene mungapezere zotulukapo zabwino koposa?