Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 8/8 tsamba 32
  • Kuchita ndi Malingaliro

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuchita ndi Malingaliro
  • Galamukani!—1991
Galamukani!—1991
g91 8/8 tsamba 32

Kuchita ndi Malingaliro

Kuchita zimenezo mwachipambano kuli kotokosa kwenikweni. Wachichepere wina akufotokoza chokumana nacho chake motere: “Ndinkadzimva wachimwemwe, koma mphindi yotsatira ndinali wopsinjika kwenikweni. Nthaŵi zina sindinakhoze ngakhale kudziŵa chomwe ndinali kulingalira. Kunali ngati kuti ndinali wotaika kotheratu mumdima. Sindikanatha kutulutsa zakukhosi kwanga ndi malingaliro anga mosasamala kanthu za amene ndinalankhula naye, osati ngakhale inemwini. Ndinkadzimva ngati kuti sindinali kupeza chisamaliro kuchokera kwa anthu ondizinga, makamaka anzanga akusukulu, chifukwa chakuti sindinali wokongola mokwanira. Potsirizira pake malingaliro onsewa anali kundipha mkati, ndipo ndinayamba kudzida inemwini ndi umunthu wanga.”

Msungwanayu anali ndi kope la bukhu la Your Youth—Getting the Best Out Of It. Iye akulemba kuti: “Ilo linali lokondweretsa kwenikweni, chotero ndinafuna kuŵerenga mutu wotsatira wakuti ‘Moving Into Womanhood’ (Kufika Kuukazi). Sindinakhulupirire zomwe ndinkaŵerenga. Mutuwo unalongosola ndendende mmene ndinali kumverera ndi chifukwa chake ndinali kumverera motero. Kunali kolimbikitsa koposa kuŵerenga kuti kunali kwachibadwa kudzimva mwanjirayi. Ndimangofunikira kudziŵa njira yolondola yochitira nazo.”

Kuwonjezera pakuthandiza achichepere kuchita ndi malingaliro awo, bukhu limeneli limafotokoza nkhani zonga ngati kugwiritsira ntchito mankhwala ogodomalitsa molakwika ndi kuyankha mafunso akuti, Kodi achichepere ayenera kumwa zakumwa zoledzeretsa? ndipo, Kodi ayenera kugonana asanakwatirane? Ngati mungakonde kulandira kope, chonde lembani ndikutumiza kapepalaka.

Ndingakonde kulandira bukhu lachikuto cholimba lamasamba 192 la Your Youth—Getting the Best Out of It. (Kunja kwa Zambia, lemberani nthambi ya Watch Tower yakwanuko kaamba ka chidziŵitso. Onani patsamba 5.)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena