Tsamba 2
MITUNDU YOGWIRIZANA Kufunafuna Kwake Mtendere Wadziko 3-10
Zochitika zachilendo zachitika posachedwapa ku Mitundu Yogwirizana, kusintha njira imene ambiri amaliwonera gululo. Kodi nchiyani chimene chachitika, ndipo kodi chingatanthauzenji kaamba ka mtsogolo?
“Kodi Nchifukwa Ninji Sindingamalize Zimene Ndayamba?” 14
Achichepere ambiri amavutika kumaliza zimene ayamba, monga ngati ntchito yapanyumba, homuweki, ndi ntchito zina. Kodi vuto limeneli lingawongoleredwe motani?
Chifukwa Chake Zaumaliseche Ziri Zaupandu 28
M’dziko limodzi pambuyo pa linzake, zaumaliseche zakhala zofalikira. Popeza kuti ziri zotchuka kwambiri, kodi zingakhaledi zaupanda kwenikweni?