Tsamba 2
Mmene Mungapiririre Mutachotsedwa Ntchito 3-10
“Anandiuza kuchotsa zinthu pa desiki langa ndikulongedza katundu wanga. Basi pompo, ndiko kunali kupita kwanga.” Ngati mwachotsedwa ntchito, kodi mungapirire motani m’zandalama ndi malingaliro? Kodi nchiyani chimene chiri chofunika koposa ndalama? Nkhani zoyambirira zidzasanthula mafunsoŵa.
Kodi Kusuta Kulidi Koipa Motero? 18
Achichepere ambiri amayamba kusuta mosasamala kanthu za kuvulaza kwake thanzi. Koma pali chifukwa chabwinopo cholekera.