Chinachake Chofunika Koposa Ndalama
“Njira yathu yosonkhezerera anthu kufikira lerolino yazikidwa kwakukulukulu pa mphotho za ndalama.”—Psychology Today.
NANCY ndi Howard adali ndi makonzedwe aakulu pamene anakwatirana mu 1989. Iwo anafuna nyumba, mwana, magalimoto atsopano, ndi tchuthi cha ku maiko akunja. Iwo anali nazo ndalama zokwaniritsa zonsezo. Koma mwadzidzidzi onse aŵiri anakhala paulova. Ndalama zomwe zinasungidwira kugula nyumba zinangogwiritsiridwa ntchito kulipira lendi.
Pochita mantha kaamba ka mtsogolo, iwo anasintha makonzedwe awo onse—kuphatikizapo a kuyamba banja. “Zaka zisanu kuchokera tsopano,” anatero Nancy, “sindikuganiza kuti tidzakhoza kubwerera paja tinali. Zonse zinapita, ndipo sindikudziŵa ngati zidzabweranso.”
Chimenechi chimasonyeza bwino motani nanga chiyambukiro choswa maganizo cha kutaikiridwa ntchito! Koma chimavumbulanso mphamvu yachinyengo ya ndalama. Zimene ziripo lero sizingakhalepo mawa. Monga momwe Baibulo limachenjezera mowona kuti: “Ndalama zako zikhoza kuzimiririka m’kamphindi, monga ngati kuti zinamera mapiko ndikuuluka ngati chiwombankhanga.”—Miyambo 23:5, Today’s English Version.
Kuvomereza mkhalidwe wakusakhala kwa ndalama nkosavuta kukunena koposa kukuchita. “Ndalama ndimuyezo wa zinthu zonse,” inatero Psychology Today ponena za maganizo ofala kulinga ku ndalama. “Timayesa zinthu kapena kuzipima ndi ndalama, kaŵirikaŵiri ngakhale ife eni.” Chilakolako champhamvu chakufuna kupeza ndalama chatsogolera ngakhale okhupuka ku nkhaŵa yopitirizabe, tondovi, ndi mavuto ena.
Kufunika kwa Nzeru
Koma pali chinachake chofunika koposa ndalama. Baibulo limachitchula pa Mlaliki 7:12 kuti: ‘Nzeru ichinjiriza monga ndalama zichinjiriza.’ Ndiyeno vesilo limawonjezerapo mfundo yonena za nzeru imene imaisonyeza kukhala yoposa ndalama kuti: ‘Nzeru isunga moyo wa eni ake.’
Nzeru imaphatikizapo kukhala wokhoza kulingalira molama pamene tiyang’anizana ndi mikhalidwe yopereka chitokoso. Pamene tiyang’anizana ndi kutaikiridwa ntchito, kulingalira kolama kuyenera kutiuza kuti mtengo weniweni wa moyo sumapimidwa ndi ndalama. Kulingalira kolama kudzatithandizanso kuika chisamaliro choyenera pa zofunika zathu zoyambirira kuti zikhale m’dongosolo lake.
Kodi Zofunika Zanu Zoyambirira Nziti?
Kodi nchiyani chimene mumaika patsogolo m’moyo wanu? Kodi ntchito yanu njofunika kwambiri koposa ukwati wanu? Kodi nyumba yanu njofunika kwambiri koposa ana anu? Kodi ndalama nzofunika kwambiri koposa thanzi lanu? Tsiku lirilonse timapanga zosankha zozikidwa pa zikhumbo zathu, zofunika zathu zoyambirira. Pamene tiyang’anizana ndi mavuto a zandalama, zofunika zoyambirira zoterozo zidzatiuza njira yochitiramo zinthu. Kodi zofunika zanu zoyambirira nzozikidwa pachiyani?
Yesu Kristu anati: “Achimwemwe ali awo ozindikira kusoŵa kwawo kwauzimu.” (Mateyu 5:3, NW) Onani kuti Yesu anasonyeza kuti uzimu uli chosoŵa, chofunika choyambirira, osati mkhalidwe wongoulondola pamene zinthu zonse m’moyo wa munthu ziribwino.
Chiri chitokoso kuika chosoŵa chauzimu chimenecho m’malo oyambirira pamene muli pavuto la kupezera banja zofunika zakuthupi. Komabe, amene amatero ali achimwemwe, monga momwe Yesu ananenera. Pamene kuli kwakuti amadera nkhaŵa za kupeza ndalama zokhalira moyo, iwo amakhalako omasuka ku “zopweteka zosaneneka za maganizo” zimene wina amavutika nazo poika ndalama patsogolo. (1 Timoteo 6:10, Phillips) Anthu otero amapezanso chitonthonzo m’mawu a Davide olembedwa pa Salmo 37:25 akuti: ‘Ndinali mwana ndipo ndakalamba: ndipo sindinapenya wolungama wasiyidwa, kapena mbumba zake zirinkupempha chakudya.’
Khutiritsani Chosoŵa Chanu Chauzimu
Chosoŵa cha munthu chauzimu nchachibadwa. Iye amafuna zoposa chakudya, chovala, ndi nyumba. Uzimu umaposa pamenepo, umapenda mafunso monga ngati, ‘Kodi nchifukwa ninji ndiri pano?’ ndipo, ‘Kodi nkuti kumene dzikoli—ndi moyo wanga—zikupita?’
Kuwopa “tsoka la zachuma” kwasonkhezera ambiri kuzindikira chosoŵa chawo chauzimu. Newsweek inasimba kuti: “Mabuku onena za maulosi—amene amamasulira zochitika zatsopano kukhala zizindikiro zonenedwa m’Baibulo za mapeto a dziko—akugulidwa pa mlingo wofikira pa 50 mpaka 70 peresenti kuposa chaka chatha.” Komabe, kuti akhutiritse chosoŵa chauzimu chimenecho, munthu ayenera kufunafuna chidziŵitso cholongosoka, osati chabe zonena za anthu.
Tikukupemphani kuti mufufuze Mawu a Mulungu, Baibulo Lopatulika. Ilo liri ndi nzeru yogwira ntchito yokuthandizani kulaka nkhaŵa za moyo. Kuposa zimenezo, Baibulo litha kukupatsani chidziŵitso cholongosoka cha zimene ‘nthaŵi zowawitsa’ zimatanthauza. (2 Timoteo 3:1) Mwakulembera ofalitsa magazini ano, phunziro Labaibulo lapanyumba laulere lingalinganizidwe. Ino ndiyo nthaŵi yoposa ndi kalelonse yakufuna nzeru yeniyeni yofunika panthaŵi ino—ndi chidziŵitso cholongosoka cha mtsogolo—kuchokera m’Mawu a Mulungu, Baibulo.
[Chithunzi patsamba 9]
Mapindu auzimu ayenera kuwonedwa kukhala amtengo wapatali