Kodi Kukhala Wowona Mtima Kumapereka Mphotho?
POWONA kusawona mtima kochuluka pakati pa achikulire, kaŵirikaŵi achichepere amatsatira chitsanzo chawo. Komabe, nkotonthoza chotani nanga—ndiponso koyenera kuzindikiridwa—mmene kuliri pamene munthu wina ali wowona mtima! Sports Illustrated inayamba chitsanzo choterocho cha kuwona mtima ndi ndemanga iyi: “Nayi nkhani yobwezeretsa chikhulupiriro cha munthuwe.”
Magaziniwo anasimba za maseŵera a chipako champira wa achichepere ku Florida, United States. Woseŵera woyamba anaimitsa ndi kumenya mpira wodzera chapansi nayesa kukhudza wothamanga wochokera kumalo oyamba kumka ku achiŵiri. Lifali, Laura Benson, anatulutsa wothamangayo, koma woseŵera woyamba anauza lifali kuti: “Adona, sindinamkhudze wothamangayo.” Choncho Benson anapatsa wothamangayo malo achiŵiri.
Mkati mwamaseŵera otsatira milungu iŵiri pambuyo pake, wachichepere mmodzimodziyo anachita zofanana. Benson analinso lifali. Panthaŵi iyi iye analingalira kuti mnyamatayo waphonya kukhudza wothamangayo, ndipo analengeza wothamangayo kukhala wopanda liwongo. Ngakhale kuti mnyamatayo sananene kanthu pobwerera kumalo ake, Benson anawona kuti kanthu kena kanalakwika mwa njira imene mnyamatayo anampenyera. Choncho iye anapita kwa mnyamatayo nafunsa kuti: “Kodi unali utamkhudza wothamangayo?”
“Inde,” iye anatero.
Benson atasintha kugamula kwake ndi kutulutsa wothamangayo, aphunzitsi agulu lolimbana ndi linalo anatsutsa. Koma iye anafotokoza zimene zidachitika milungu iŵiri yapitayo naati: “Ngati wachichepere ali wowona mtima motero, ndiyenera kumupatsa mpirawo.”
Osawona mtima amawonekera kukhala akupambana m’dziko lerolino. Ziridi monga momwe wamasalmo Wabaibulo analembera nthaŵi ina kuti: “Tapenyani, oipa ndi aŵa; ndipo pokhazikika chikhazikikire awonjezerapo pa chuma chawo.” (Salmo 73:12) Komabe, kunena zowona kuwona mtima potsirizira pake kumapereka mapindu abwino koposa. Kumapezera munthu ulemu wa anthu anzake. Koma zofunika koposa, kumampezera chiyanjo cha Yehova Mulungu, amene angafupe munthuyo ndi moyo wosatha.