Makope 15,290,000 A Kope Lirilonse m’Zinenero 110
Nsanja ya Olonda iri mosayerekezeka magazini achipembedzo ofalitsidwa koposa padziko lonse. Kunena zowona, ali magazini ochepekera amtundu wake amene aposa kufalitsidwa kwake. Kodi nchifukwa ninji imaŵerengedwa mofala chotero?
Imalongosola mmene dziko latsopano lolungama posachedwapa lidzakhazikitsidwira, ikumapatsa oŵerenga ake chiyembekedzo chotsimikizirika ndipo chowona kaamba ka mtsogolo. Kodi mungakonde kuti Nsanja ya Olonda itumizidwe kunyumba kwanu? Ngati kuli choncho, chonde dzazani ndi kutumiza katikiti kotsatiraka.
Ndingakonde kuti magazini a Nsanja ya Olonda atumizidwe kunyumba kwanga. (Kunja kwa Zambia, lemberani nthambi ya Watch Tower yakwanuko kaamba ka chidziŵitso. Onani tsamba 5.)