Chothandiza Pokula
Kukulira m’nthaŵi zovuta zino sikopepuka. Achichepere amayang’anizana ndi mikhalidwe yambiri yatsopano ndipo amafunikira kupanga zosankha zazikulu. Kodi ndiyenera kusuta? Kulandira mankhwala oledzeretsa? Kodi ndimakhalidwe otani amene ali oyenera kwa wosiyana naye ziŵalo? Bwanji ponena za psotopsoto ndi kugonana kwa ofanana ziŵalo? Wachichepere wina analemba kuti:
“Ndine wazaka pafupifupi 13 tsopano, ndipo ndingofuna kukuthokozani kaamba ka bukhu la Youth. Bukhuli landithandiza kwambiri m’masiku ano ovuta kukuliramo. Ndingokhumba kuti achichepere onse amsinkhu wanga ndi okulirapo anadziŵa za bukhu limeneli.”
Bukhuli, limene limayankha mafunso onse ali pamwambapa ndi ena ambiri, ndilo Your Youth—Getting the Best Out Of It. Ngati mungafune kulandira kope, chonde dzazani ndi kutumiza kapepalaka.
Ndingakonde kulandira bukhu lachikuto cholimba lamasamba 192 la Your Youth—Getting the Best Out Of It. (Kunja kwa Zambia, lemberani nthambi yakumaloko ya Watch Tower kaamba ka chidziŵitso. Onani tsamba 5.)