Tsamba 2
Nkhaŵa za Ndalama—Kodi Zidzathadi? 3-8
“Ndalama nzofunika,” analemba tero Galbraith, katswiri wa zachuma. “Zimalingana ndi chikondi monga magwero aakulu koposa a chimwemwe cha munthu. Ndipo zimalingana ndi imfa monga magwero aakulu koposa a nkhaŵa yake.” Dongosolo lazachuma lamakono limadzetsa maupandu, nkhaŵa ndi zikhumbo. Nkhani zathu zoyambirira nzimene zipanga Gawo 1 m’mpambo wa magawo 6 m’miyezi itatu yotsatira amene adzafotokoza mbiri ya dongosolo lamalonda ndi ntchito ya ndalama m’chitukuko cha anthu.
Kukwatirana Kapena Kukhalira Pamodzi—Kodi Choyenera Nchiti? 30
Mamiliyoni ambiri lerolino amasankha kukhalira pamodzi popanda mapindu a ukwati. Kodi lingaliro la Baibulo pa nkhaniyi nlotani?
[Mawu a Chithunzi patsamba 2]
With kind permission of the Kunsthistorisches Museum, Vienna