Pamene Ziyembekezo za Mtendere Zinasweka
PANALI anthu ochepa kwambiri amene anayembekezera kuti 1914 ikakhala chaka chapadera. Ndiiko komwe, mtsogolo munawoneka kukhala moŵala kwa anthu koposa m’zaka zinapitapozo. Sayansi inali kupita patsogolo m’kugonjetsa matenda. Bwanji ponena za nkhondo? Eya, monga momwe nyuzipepala ya ku Vatican yotchedwa L’Osservatore Romano inanenera mu February 1991, 1914 isanafike anthu “anakhulupirira kuti nkhondo inakhala mbiri yakale” ndikuti munthu pomalizira pake anali kukhala mu “nyengo imene nkhondo inaletsedwa ndi anthu otsungula ndi maboma.”
Komabe, 1914 ndi zaka zotsatirapo zinasungira anthu okhutiritsidwa molakwa ndi mkhalidwewo zodabwitsa zowopsa. Choyamba chinali nkhondo yotchedwa Nkhondo Yaikulu ya 1914-18 imene inaswa ziyembekezo za mtendere. Kwenikweni, L’Osservatore Romano inaitcha “kupha kwakukulu koyamba m’mbiri yamakono, kosonkhezeredwa ndi, pakati pa zinthu zina, zotumbidwa zasayansi zimene asayansi a mibadwo yakale anakhulupirira kuti zinali ndi zolinga zodzetsa mtendere.” Nkhondoyo inachititsa manyazi sayansi monga njira yolephera kudzetsa mtendere; mmalomwake, sayansi inatheketsa nkhondo kupha chiŵerengero cha anthu choposa ndi kalelonselo.
Ndipo pamene kupha kwa nkhondoyo kunatha, kupha kwina kunayamba. Fuluwenza ya Spanya ya 1918-19 inapha anthu oposa 20 miliyoni—kupambana kutalitali pa ophedwa ndi Nkhondo Yaikulu yeniyeniyo. Panali kuyesayesa kosaphula kanthu; kufalitsa matendawo kunalengezedwa kukhala upandu m’maiko ena. Apolisi anagwira ngakhale amene anayetsemulira pakati pa anthu! Koma sizinaphule kanthu. Mofanana ndi namondwe, nthendayo inasesa miyoyo mosaletseka kufikira pamene inatha iyo yokha. Mizinda yathunthu inapululutsidwa. Mitembo inaunjikidwa m’mamotchale a m’mizinda.
Nyengo yakusintha imene inafika mu 1914 inasokoneza munthu. Maloto ake akuchotsapo nkhondo ndi matenda, ziyembekezo zake za dziko lamtendere lochititsidwa ndi nzeru zaumunthu, zinalephera mochititsa chisoni. Ndipo pamene zinthu zinapitiriza kuipirako, pamene Nkhondo Yaikulu inayenerera kutchedwa Nkhondo Yadziko ya I chifukwa cha yoipambanayo, Nkhondo Yadziko ya II, pamene matenda, umphaŵi, njala, ndi kusayeruzika zinapitiriza kubuka monga miliri yaikulu kuzungulira padziko, olemba mbiri anayamba kuzindikira 1914 kukhala posinthira m’mbiri ya anthu.
Koma mosiyana ndi dziko lonse, Ophunzira Baibulo Amitundu Yonse (monga momwe Mboni za Yehova zinadziŵikira panthaŵiyo) anayembekezera 1914 kukhala chaka chosinthirapo kwa nthaŵi yaitali chisanafike. Ndipo m’zaka zonsezi kuyambira pamenepo, Mboni za Yehova sizimadabwa powona kunyonyotsoka kumene dziko lagweramo lerolino. Maulosi Abaibulo awathandiza iwo kuyembekezera zochitika zimenezi ndipo ngakhale kuwona nthaŵi yaulemerero yoyembekezeredwa mtsogolo. Kodi zimenezo nzotheka motani? Pamene Mboni za Yehova zidzakuchezeraninso, mungakonde kuzifunsa ponena za zimenezi. Kapena mukhoza kulembera ofalitsa magazini ano.
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
Redrawn from artwork of Franklin Booth