Tsamba 2
Maphunziro Azakugonana—Kodi Ndani Ayenera Kuwapereka? 3-11
Ana amasonyezedwa zakugonana m’njira zosiyanasiyana lerolino. Koma zimene amaphunzitsidwa kaŵirikaŵiri zimakhala zolakwa ndipo zikhoza kuwawononga. Kodi ndimotani mmene makolo angaphunzitsire ana awo moyenera ponena za kugonana? Kodi ayenera kuyamba liti? Nkhani zotsatira zidzakhala zothandiza kwa inu.
Kuthandiza Okhala ndi Vuto Lakadyedwe 12
Mamiliyoni a anthu amakhala ndi vuto lakadyedwe. Bwanji ngati lagwira chiŵalo cha banja lanu kapena bwenzi lanu? Ziripo njira zothandiza zimene mungatsatire.
Kusintha kwa Maindasitale—Kodi Kwatsogolera ku Chiyani? 16
Kwadzetsa njira zamakono zochitira zinthu mosavuta ndi maubwino ena ambiri. Komabe kuli ndi mbali zake zoipa. Tadziŵerengerani mudziŵe mmene zinakulitsira ukapolo ndikudzetsa nkhondo zokhetsa mwazi wochuluka.
[Mawu a Chithunzi patsamba 2]
The Old Print Shop/Kenneth M. Newman