Chochitika Chapadera Kodi Mudzabwera?
MONGA akapolo oponderezedwa mu Igupto zoposa zaka 3,500 zapitazo, Aisrayeli anafunitsitsa chilanditso. Koma Farao anakana kulola akapolo ake kuchoka. Chotero Yehova Mulungu anauza Aisrayeli kupha mwana wankhosa ndi kupaka mwazi wake pamphuthu ya nyumba zawo. Usiku womwewo mngelo Wake anapitirira nyumba zokhala ndi mwazi pamphuthu koma anapha ana aamuna oyamba kubadwa a nyumba zonse za Aigupto. Pamenepo Farao anamasula Aisrayeli. Chiyambire pamenepo, patsiku lapachaka pamene mngelo anapitirira nyumba za Aisrayeli, Ayuda amakumbukira chochitikachi.
Pambuyo pake, Yesu Kristu anabwera padziko lapansi. Tsiku lina Yohane Mbatizi, amene anabatiza Yesu, anasonya kwa iye nati: ‘Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi!’ (Yohane 1:29) Monga momwe mwazi wa mwana wa nkhosa wa Paskha unatanthauza chilanditso kwa mwana woyamba kubadwa Wachiisrayeli, momwemonso mwazi wokhetsedwa wa Kristu ukhoza kutipulumutsa ku tchimo ndi imfa.
Yesu anakhazikitsa phwando la chakudya chokumbukira imfa yake yansembe. Iye anapatsa atumwi ake okhulupirika mkate nati: ‘Tengani, idyani; ichi ndi thupi langa.’ Ndiyeno anaŵapatsa chikho cha vinyo nati: ‘Mumwere ichi inu nonse, pakuti ichi ndicho mwazi wanga wa pangano, wothiridwa chifukwa cha anthu ambiri ku kuchotsa machimo.’ Ndiponso, Yesu anati: ‘Chitani ichi chikumbukiro changa.’ (Mateyu 26:26-28; Luka 22:19, 20) Chotero Yesu anatanthauza kuti icho chikhale chikumbukiro chapachaka cha imfa yake.
Mboni za Yehova zikukuitanani mwachimwemwe kugwirizana nazo pochita phwando la Chikumbutso limeneli. Mukhoza kufika pa Nyumba Yaufumu yakufupi kwambiri ndi kwanu. Funsani Mboni za Yehova zakwanuko ponena za nthaŵi yeniyeni ndi malo. Deti la phwandolo mu 1992 ndi Lachisanu, April 17.