Tsamba 2
Thandizani! Ndife Alendo 3-12
Pafupifupi dziko lirilonse liri ndi alendo—anthu mamiliyoni ambiri osamuka kwawo. Angakhale akugwira ntchito pamodzi nanu kapena kusamukira kwanuko. Mwatsoka lanji, amawonedwa kaŵirikaŵiri kukhala chiwopsezo. Koma nkhani iriyonse imakhala ndi mbali ziŵiri nthaŵi zonse. Chotero, kodi nchifukwa ninji amasamuka? Kodi alidi chiwopsezo? Kodi nchiyani chomwe mungachite kuwathandiza?
Kodi Nchifukwa Ninji Ndiyenera Kufika Msanga Panyumba? 28
Mwachiwonekere achichepere akufunsa funso limeneli padziko lonse. Chotero nchifukwa ninji makolo amakhazikitsira ana awo nthaŵi yausiku yoyenera kufika panyumba?