Kodi Mudzalabadira Uphungu wa Dokotala?
KODI dokotala ali ndi thayo lanji pankhani ya kusuta fodya? Kodi angofunikira kupereka mankhwala kwa odwala matenda ochititsidwa ndi kusuta? Dr. Louis Sullivan, mlembi wa Dipatimenti ya Zaumoyo ndi Mautumiki a Anthu ya ku United States, akulingalira kuti adokotala ayenera kuchita zambiri kuposa zimenezo. Posachedwapa iye analemba mu The Journal of the American Medical Association kuti: “Asing’anga ali ndi thayo lakudziŵitsa odwala maupandu a kusuta, kuthandiza odwala amene sasuta kuti asayambe kusuta, ndi kuthandiza amene amasuta kuleka chizoloŵezicho.”
Kodi nchifukwa ninji adokotala ayenera kudziloŵetsamo motero m’miyoyo ndi zosankha za odwala awo? Dr. Sullivan akuvomereza kuti: “Kusuta kuli chosankha, koma nchosankha choipa.” Iye akupereka umboni wamphamvu uwu: “Chaka chirichonse, kusuta kumapha nzika za Amereka pafupifupi 400 000; chimenecho nchiŵerengero cha anthu oposa 1000 patsiku, kuchititsa imfa zoposa imodzi mwa imfa zisanu ndi imodzi za m’dziko lathu. Chiŵerengero cha nzika za Amereka zimene zimafa chaka chirichonse ndi matenda ochititsidwa ndi kusuta chimaposa chiŵerengero cha nzika za Amereka zimene zinafa m’Nkhondo Yadziko ya II.”
Akumasumika maganizo pa akazi, Sullivan akutchula zopezedwa zina zosokoneza maganizo: “Kansa ya m’mapapo yakhala chochititsa imfa chachikulu mwa akazi kuposa kansa ya m’maŵere. Akazi amene amasuta ali othekera kukhala ndi matenda a mtima kuwirikiza katatu kuposa akazi omwe sanasutepo, ndipo akazi osuta amadziika paupandu wakukhala ndi umoyo wamatenda ndi imfa yochititsidwa ndi emphysema [kutupa mapapo] ndi matenda ena ochititsidwa ndi kusuta. Akazi amene amasuta ali ndi pathupi ali othekera kwenikweni kupititsa padera, kukhala ndi makanda a sikelo yotsika, ndi ana amene amamwalira paubwana.”
Mosasamala kanthu za mfundo zowopsa zimenezi, Dr. Sullivan akunena kuti padakali chitsenderezo chachikulu pa anthu cha kusuta. Iye akutsutsa kuti njira zosatsira ndudu, zosumika maganizo pa achichepere “nzonyansa.” Ndiponso akuchita mantha ndi kugwiritsira ntchito kwamachenjera kwa zitsanzo za achichepere okongola, okhala m’malo owala kupereka kwa achichepere lingaliro lakuti kusuta nkwabwino ndi kosangalatsa. Kwenikweni, ngati kuchuluka kwa kusuta sikuchepekera, ana mamiliyoni asanu omwe ali ndi moyo lerolino adzafa ndi matenda ochititsidwa ndi kusuta. Dr. Sullivan akusonkhezera adokotala anzake kuti: “Limenelo ndilo tsoka limene tiyenera kuliletsa.”
Kaya adokotala adzaletsadi tsoka limeneli zidakali zokaikitsa. Monga momwe Dr. Sullivan akunenera kuti: “Mwatsoka, asing’anga ena amapitirizabe kusuta, kupereka chitsanzo choipa kwa odwala awo ndi ogwira ntchito namapereka uthenga wotsutsa za umoyo kwa onse amene amawadziŵa.”