‘Kunyonyosoka kwa Makhalidwe m’Masukulu Apamwamba’
“KWA miyezi 6 yapitayo kagulu ka openda maakaunti kakhala kakupenda mosamalitsa maakaunti a mayunivesite otchuka 14 a dziko la [U.S.A.], kakumafunafuna ndalama zimene boma latchajidwa ‘mosadziŵa.’ ‘Tinapeza kuti masukulu 14 anaphatikizapo $20.4 miliyoni a U.S.A. a mitengo yosaloleka’” ndizo zimene openda maakaunti anagwidwa mawu kukhala akunena m’lipoti lofalitsidwa m’magazini a ku Britain otchedwa New Scientist a January 25, 1992.
Openda maakaunti aboma anapita kukafufuza chaka chatha pamene kunadziŵika kuti Yunivesite ya Stanford inagwiritsira ntchito ndalama za okhoma misonkho zokwanira $25 miliyoni a U.S.A. Zophatikizidwa zinali zowonongedwa zonga maluwa aaŵisi atsiku ndi tsiku a kunyumba ya pulezidenti wa yunivesiteyo, phwando laukwati, kukwera mtengo kwa ngalawa yokongola, ndalama zolipiridwa ku kalabu yakumidzi, ndi kuyendetsa malo amasitolo. Atayang’anizana ndi zenizeni zosakondweretsa zimenezi, pulezidenti wa Stanford wapanthaŵiyo, Donald Kennedy, ananena kuti akathesa “ndalama zowonongedwa zimene sizimadziŵika bwino ndi anthu onse” ndipo mwakutero “kupewa chisokonezo chirichonse chimene chingakhalepo.” Boston Herald, ya January 1, 1992, popereka ndemanga za yankho lake, inati: “Mwamawu ena, vuto lokha linali lakuti khwimbi la opulukira kunja kwa malo ayunivesiteyo lingakhale losakhoza kuzindikira zimene aphunzitsi olemera anali kuchita m’maphunziro.”
Panali pambuyo pa mavumbulutso amenewa onena za Stanford kuti openda maakaunti a boma la United States anatumizidwa paulendo wawo waposachedwapa kwambiri woyendera mayunivesite 14 natulukira kuwawanyidwa kwa ndalama zina zokwanira $20.4 miliyoni a U.S.A. Ophatikizidwa anali mayunivesite otchuka onga Yunivesite ya Michigan, ya Johns Hopkins, ya Yale, ndi ya Emory. Zoti zilipiridwe zopemphedwa ndi mayunivesite 14 amenewo zinaphatikizapo zinthu zonga “ndalama zolipilira ndege za akazi a mapulezidenti; ndalama zolipilira ndege kumka ku Grand Canyon kukafika pamsonkhano wa oikizira; ndalama zambirimbiri zolipilira kukafika pamasewera ampira; zolipilira wolankhula nthabwala paphwando la Krisimasi; ndi kulipilira kukhala ziwalo za magulu a masewera olimbitsa thupi a payunivesite ndi makalabu amasewera osiyanasiyana ophatikizapo kalabu yokayendetsa ngalawa zokongola zokwera mtengo.”
Pamene openda aboma analengeza kuti akapitanso ku M.I.T. (Massachusetts Institute of Technology) ndi ku Harvard, kuchepetsa kwakukulu kunalengezedwa ndi masukulu amenewa. M.I.T. inachepetsa ndalama zokwanira $731,000 a U.S.A. pazopempha zawo kaamba ka mafufuzidwe; Harvard inachepetsa ndi ndalama zokwanira $500,000 a U.S.A. pandalama zake zolipilirazo. Duke inapeza “zolakwa zochitidwa mosadziwa” pa zimene inali kutchaja. California Institute of Technology inasankha kuti sikatchajanso boma kaamba ka kukhala kwake chiwalo cha kalabu yakumidzi. Yunivesite ya Pittsburgh sinakhoze kutenga ndalama za okhoma msonkho kuti ilipilire matikiti a masewera kapena matikiti a pulezidenti ndi mkazi wake olipilira matikiti andege popita ku Grand Cayman Island.
“Kunyonyosoka kwamakhalidwe,” inatero The Boston Herald, “nkwakukulu kwambiri koposa nkhani zandalama. Zimenezo zangokhala ngati pamene munthu anagubuduza mwala ndi kulola anthu onse kuwona zimene zinali kukwawa pansi pake. . . . Kuwawanya ndalama pa Stanford ndi masukulu ena otchuka nkosanunkha kanthu kaamba ka ziwerengero za ndalama zophatikizidwa koma kuti ndiko chizindikiro cha kulephera kwakukulu kwa makhalidwe. Kukwiya kwa anthu onse kokha ndi masinthidwe amasukuluwo ndizo zimene mwinamwake zingaimike chikhotererocho.”