“Linangolembedwera Ine Basi”
ZIMENEZO ndizo zimene wachichepere wina wa ku St. Lucia ku West Indies ananena ponena za bukhu lakuti Your Youth—Getting the Best Out Of It. “Pamene ndinafika pamutu 5,” anafotokoza motero msungwanayo, “ndinawona kuti chidziwitsocho chinangolembedwera ine basi. Chinali chonena za kuchita psyotopsyoto ndi kugonana kwa ofanana ziwalo.
“Kuchita psyotopsyoto kwakhala limodzi la mavuto anga aakulu. Kwazaka zitatu ndakhala ndikumenyera nkhondo kukugonjetsa. Ndinafika ngakhale polingalira kuti ndinali ndekha padziko lonse amene akuchita zimenezo. Ndikuthokoza Mulungu kupangitsa anthunu kulemba bukhu lamtengo wapatali limeneli limene linandipatsa uphungu wa zimene ndiyenera kuchita. Ndikugwiritsira ntchito zothetsera zanu.
“Vuto langa lachiwiri nlonena za mabwenzi achinyamata. Ndayang’anizana ndi zogwiritsa mwala zambiri pankhaniyi. Bwenzi langa lachinyamata lotsiriza liri ndi bwenzi lina lachisungwana, ndipo kukuwonekera ngati akumkonda koposa ine. Sindidziwa chochita.
“Komabe, ndiyenera kunenapo mawu, kuti pamene ndapweteketsedwa mtima ndi mabwenzi anga, makamaka bwenzi langa lachinyamata, ndimangotenga kabukhuka ndi kukawerenga. Kakhala chithandizo chachikulu kwa ine. Kandipatsa uphungu wambiri umene sindinaganizire. Nditawerenga mitu yambiri ya kabukhu kofiiraka, ndinangokhala pansi ndi kulira. Ndinatonthozedwadi ndi kutsitsimulidwa ndi mutu 8 ndi 23.”
Kukula m’nthaŵi zovutazi ndithudi sikofewa. Achichepere akuyang’anizana ndi mikhalidwe yatsopano yambiri ndipo ayenera kupanga zosankha zazikulu. Kusuta kodi? Kuvomereza anamgoneka kodi? Kodi ndikudzisungira kotani kumene kuli koyenera ndi mmodzi wa osiyana nawo ziwalo? Ngati mungakonde kukhala ndi chidziwitso chowonjezereka kapena phunziro Labaibulo lapanyumba laulere, chonde lemberani Watch Tower, Box 21598, Kitwe, kapena ku keyala yoyenerera yondandalitsidwa patsamba 5.