Tsamba 2
Nthenda ya Chronic Fatigue Syndrome—Mmene Mungachitire Nayo 3-15
Ambiri akudwala nthenda yosadziŵika imene posachedwapa inapatsidwa dzina lakuti CFS (chronic fatigue syndrome). Kodi nchifukwa ninji dzinalo liri losayenera? Kodi CFS ndinthenda yeniyeni? Kodi chimene chimaiyambitsa nchiyani, ndipo ndimotani mmene odwala angachitire ndi vutolo?
Kodi Cholakwa Nchiyani ndi Kulankhuzana? 18
Kodi kukambitsirana nthaŵi zonse ndi munthu wina, ngakhale ngati kumachitidwira pafoni, kungakhale kupalana ubwenzi? Kodi kufulumira kupalana ubwenzi kuli ndi maupandu otani?