Tsamba 2
Kodi Pali Mtsogolo Motani kwa Ana? 3-9
Ana zikwi zambiri amafa tsiku lirilonse chifukwa cha matenda kapena kudya mosakwanira. Kodi pali chiyembekezo chotani chakuti ana owonjezereka angakhale ndi moyo wachimwemwe, wotetezereka mtsogolo?
Kuloŵedwa ndi Ululu wa Mtovu—Kodi Inu ndi Ana Anu Muli Paupandu? 21-30
Mtovu uli konsekonse m’malo athu otizungulira, ndipo asayansi akupeza kuti ngakhale mlingo wochepa kwambiri wa chitsulo m’thupi la munthu umakhala chiwopsezo chachikulu kuumoyo—makamaka kwa ana. Kodi nchiyani chimene chingachitidwe kudzitetezera ife eni ndi ana athu?