Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g93 2/8 tsamba 32
  • “Inu Mumaderadi Nkhaŵa Anthu”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Inu Mumaderadi Nkhaŵa Anthu”
  • Galamukani!—1993
Galamukani!—1993
g93 2/8 tsamba 32

“Inu Mumaderadi Nkhaŵa Anthu”

Anagamula motero mwamuna wina wa ku California, U.S.A., wokonda kuŵerenga mabuku a Watch Tower Society. Ponena za bukhu lakuti The Greatest Man Who Ever Lived, iye akulemba kuti:

“Tsopano ndikuliŵerenga kachiŵirinso, ndipo silitopetsa konse kuliŵerenga. Bukhulo siliri lopatsa chidziŵitso chabe komanso zithunzithunzi zake zamawonekedwe okongola zimawoneka ngati zamoyo. Chithunzithunzi chirichonse chimandichititsa kudziyesa kuti ndiri m’nthaŵi ya Yesu.

“Mwachitsanzo, mwamuna wogwidwa ndi ziŵanda pachithunzithunzi cha m’mutu 45 ndithudi akuwoneka kukhala wokwiya ndi wowopsa. Komabe Yesu wasonyezedwa kukhala akubwera kumtunda mopanda mantha natulutsa mizimu yauchiŵandayo . . .

“Zithunzithunzi zonse za atsogoleri achipembedzo aukali Achiyuda zinajambulidwadi mwaukatswiri. Zimasonyeza mmene munthu angawonekere kukhala wokwiya pamene akuyang’anizana ndi kuchita ndi Yesu komano osasiya njira zake zauchimo. Ndikhoza kunena zambiri. . . . Inu mumaderadi nkhaŵa anthu . . .

“Sindine mmodzi wa Mboni za Yehova koma ndimakonda kulandira Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Ndimayembekezera kope lirilonse mwachimwemwe, ndipo litabwera, limakhala mbali yabwino koposa ya makalata anga onse olandiridwa patsikulo. Galamukani! ya July 8 inapambana zonse! Nkhani za ‘Kulera Ana’ zinalidi zapanthaŵi yake. . . .

“Ndiri ndi zaka zakubadwa 35 ndipo ndafikira pakuzindikira kuti dziko lakaleli liri m’mavuto aakulu. Ndine wokondwa kuti mulipo kumalifotokoza monga mmene liriri ndi mmene Mulungu amaliwonera.”

Mboni za Yehova ndizo gulu la m’mitundu yonse la ophunzira Baibulo oposa mamiliyoni anayi amene ali odzipereka kuthandiza anthu kuphunzira zowonjezereka ponena za zifuno za Mulungu. Ngati mungakonde kudziŵa zowonjezereka kapena phunziro Labaibulo lapanyumba laulere, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 33459, Lusaka 10101, kapena ku keyala yoyenerera pa ondandalitsidwa pa tsamba 5.

[Chithunzi patsamba 32]

THE GREATEST MAN WHO EVER LIVED

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena