Kulinganiza Banja Kukukhala Nkhani ya Padziko Lonse
“Kulinganiza banja kungabweretse mapindu owonjezereka kwa anthu owonjezereka pamtengo wotsika koposa ‘luso la zopangapanga’ limodzi lirilonse limene tsopano liri lopezeka kufuko la anthu. . . . Zimenezi zingakhalebe zowona ngakhale ngati panalibe chinthu chotchedwa kuti vuto la kuchuluka kwa anthu.”—The State of the World’s Children 1992.
M’NTHAŴI zapita kunali kulingaliridwa kukhala kolakalakika kukhala ndi ana ambiri. Pafupifupi zaka zikwi zinayi zapitazo, pamene Rebeka anali pafupi kuchoka ku Mesopotamiya kukakwatibwa ndi Isake, amake ndi mbale wake anamdalitsa mwamawu akuti: “Mlongo wathu ndiwe, iwe ukhale amayi wa anthu zikwizikwi.” (Genesis 24:60) Nthaŵi zasintha. Lerolino, akazi owonjezerekawonjezereka akunena kuti akufuna ana ocheperapo.
“Ndinali wachitatu mwa ana asanu ndi aŵiri,” anatero Bu, mayi wazaka 22 zakubadwa wa ku Indonesia wokhala ndi mwana mmodzi wamkazi. “Atate anali wopanga ndi kugulitsa uchema m’Klaten, Central Java, ndipo makolo anga anavutika kwambiri kuyesayesa kulera ana ambiri chotero. . . . Nkosavutirapo kulera banja ngati uli ndi ana oŵerengeka chabe.”
Mawu a Bu ngofanana ndi a makolo kuzungulira padziko lonse. Mowonjezerekawonjezereka, okwatirana amafuna kulinganiza nthaŵi ya kuyamba kukhala ndi ana, chiŵerengero chawo, mpata wa kusiyana kwa misinkhu, ndi nthaŵi ya kuleka. Zimenezi zikusonyezedwa m’ziŵerengero za UN zosonyeza kuti kugwiritsira ntchito modzifunira njira zopewera kutenga mimba m’maiko osatukuka kwakula kwambiri, kuyambira pa 10 peresenti ya okwatirana mu ma 1960 kufikira ku 51 peresenti lerolino.
Maboma nawonso ali okondweretsedwa mwapadera m’kupititsa patsogolo kulinganiza banja. Yoposa theka ya maiko osatukuka akuchita maprogramu ochepetsa kukula kwa chiŵerengero cha anthu. Population Fund ya gulu la UN likuyerekezera kuti chiwonkhetso cha ndalama zowonongedwera pa maprogramu olamulira chiŵerengero cha anthu tsopano ndicho pafupifupi U.S.$4,500,000,000 pachaka. Kuti afikire zofunika zamtsogolo, akatswiriwo akuyerekezera kuti chiŵerengerochi chidzaŵirikiza podzafika chaka cha 2000.
Kodi nchifukwa ninji maiko ndi anthu paokha ali okondwerera kwambiri kuchepetsa milingo ya kubala ana? Ndipo kodi lingaliro Lachikristu nlotani pankhani yofunika imeneyi? Nkhani ziŵiri zotsatirapozi zidzalingalira mafunso ameneŵa.