Ana—Kodi Ndiwo Mapindu Kapena Mavuto?
NKHANI ya kulinganiza banja njogwirizanitsidwa kwambiri ndi chimene kaŵirikaŵiri chikutchedwa kuti bomba la kuchuluka kwa chiŵerengero cha anthu. Mkati mwa nthaŵi ya mbiri ya anthu, kukula kwa chiŵerengero cha anthu kunali kochedwa pang’ono; chiŵerengero cha akufa chinali pafupifupi chofanana ndi chiŵerengero cha obadwa. Potsirizira, pafupifupi m’chaka cha 1830, chiŵerengero cha padziko lonse chinafikira anthu mamiliyoni chikwi chimodzi.
Ndiyeno panadza kupita patsogolo m’zamankhwala ndi zasayansi kumene kunachepetsa imfa zochititsidwa ndi matenda, makamaka nthenda za ana. Podzafika mu 1930, chiŵerengero cha anthu chinali mamiliyoni zikwi ziŵiri. Podzafika mu 1960, ena mamiliyoni chikwi chimodzi anali atawonjezereka. Podzafika mu 1975, panali enanso mamiliyoni chikwi chimodzi. Podzafika mu 1987, chiŵerengero cha anthu cha padziko lonse chinafikira mamiliyoni zikwi zisanu.
Kupenda mkhalidwewo mwanjira ina, chiŵerengero cha anthu paplanetili pakali pano chikuwonjezereka pamlingo wa pafupifupi anthu 170 pamphindi iriyonse. Zimenezo zikuwonjezera pafupifupi anthu 250,000 tsiku lirilonse, okwanira kudzaza mzinda waukulu mwachikatikati. Zimenezi, zikutanthauzanso kuti, chaka chirichonse chimabweretsa chiwonjezeko cha anthu oposa mamiliyoni 90, chofanana ndi a Canada atatu kapena chofanana ndi nzika za ku Mexico. Yoposa 90 peresenti ya chiwonjezeko chimenechi ikuchitika m’maiko osatukuka, kumene 75 peresenti ya nzika za padziko lonse zikukhalako kale.
Maboma Ophatikizidwa
Koma kodi nchifukwa ninji maboma ali ofunitsitsa kuchepetsa kukula kwa chiŵerengero cha anthu mwa kulinganiza banja? Dr. Babs Sagoe, wa National Program Officer wa UN Population Fund wa ku Nigeria, akuyankha funsoli mwa fanizo lofeŵa mwa limene, akuchenjeza kuti, liri ndi chikhoterero cha kufeŵetsa mopambanitsa mkhalidwe wocholowana ndi wodzutsa mkangano. Iye akufotokoza kuti:
‘Tinene kuti mlimi ali ndi munda wa mahekitala anayi. Ngati ali ndi ana khumi ndipo akuŵagaŵira mundawo mofanana, mwana aliyense adzakhala ndi pafupifupi hafu ya hekitala. Ngati aliyense wa anawo ali ndi ana khumi ndipo akugaŵa mundawo mofananamo, aliyense wa ana awo adzakhala ndi 0.04 chabe ya hekitala. Mwachiwonekere, anaŵa sadzakhala olemera mofanana ndi agogo awo, amene anali ndi munda wa mahekitala anayi.’
Fanizoli likugogomezera unansi wa pakati pa chiŵerengero chomakulakula cha anthu ndi dziko lathu lokhala ndi polekezerali lokhala ndi chuma chochepa. Pamene chiŵerengero cha anthu chiwonjezereka, maiko osatukuka ambiri akuvutika kuthana ndi ziŵerengero za anthu zatsopanozi. Talingalirani ena a mavutowo.
Chuma. Pamene chiŵerengero cha anthu chiwonjezereka, pamakhala kufunika kwakukulu kwa nkhalango, nthaka yachonde, minda yadzinthu, ndi madzi abwino. Chotulukapo nchiyani? Magazini a Populi akudandaula kuti: “Maiko osatukuka . . . kaŵirikaŵiri amakakamizika kugwiritsira ntchito mopambanitsa chuma chadziko chimene chitukuko chawo chamtsogolo chimadalirapo.”
Zinthu. Pamene chiŵerengero chakutichakuti cha anthu chikukula, maboma amakupeza kukhala kovuta mowonjezereka kugaŵira nyumba zokwanira, masukulu, nyumba zaukhondo, misewu, ndi zipatala. Pokhala otsenderezedwa ndi mitolo yoŵirikiza ya ngongole zazikulu ndi kuchepachepa kwa chuma, maiko osatukuka akutsenderezedwa kwambiri kusamalira zosowa za ziŵerengero za anthu ziripozi, koposa kotani ngati ziri zokulirapo koposa.
Ntchito yolembedwa. Bukhu la UN Population Fund lakuti Population and the Environment: The Challenges Ahead likufotokoza kuti m’maiko osatukuka ambiri, 40 peresenti ya antchito ali kale malova. M’maiko onse osatukuka, anthu oposa mamiliyoni mazana asanu kaya ali malova kapena amagwira ntchito yaganyu, chiŵerengerocho chiri pafupifupi chofanana ndi cha antchito onse a m’maiko otukuka.
Kutetezera ziŵerengerozi kuipiraipira, maiko osatukuka ayenera kuyambitsa ntchito zatsopano zoposa mamiliyoni 30 chaka chirichonse. Anthu amene adzafunikira ntchito zimenezi ali moyo lerolino—ndiwo ana atsopano. Akatswiri akulankhula kuti ulova wa anthu ambiri ungatsogolere kunkhondo yachiweniweni, umphaŵi woipiraipira, ndi kuwonongedwa kowonjezereka kwa chuma cha m’nthaka.
Mposadabwitsa kuti maiko osatukuka owonjezerekawonjezereka akulimbikira kupititsa patsogolo kulinganiza banja. Akumaperekera ndemanga pa zimene ziri mtsogolo, mkonzi wa magazini azamankhwala a ku Briteni otchedwa Lancet anafotokoza kuti: “Chisonkhezero cha chiwonjezeko m’chiŵerengero [cha anthu], cholekezera kwakukulukulu kumaiko aumphaŵi koposerapo a dziko, chikuwonjezera kwadzawoneni ntchito imene akuyang’anizana nayo. . . . Mamiliyoni ambiri adzakhalabe osaphunzira, malova, opanda nyumba zabwino ndi osakhoza kupeza chisamaliro chochepa chamankhwala, mautumiki azamakhalidwe ndi azaukhondo, ndipo kuwonjezereka kwa chiŵerengero cha anthu kosachepetsedwa ndiko chochititsa chachikulu cha mavutowo.”
Mabanja Ophatikizidwa
Kukhazikitsa zonulirapo ndi kuyambitsa maprogramu olinganiza banja pamlingo wa dziko ndiko nkhani ina; kukhutiritsa anthu onse ndiko nkhani inanso. M’zitaganya zambiri malingaliro amwambo oyanja mabanja aakulu adakali amphamvu. Mwachitsanzo, mayi wina wa ku Nigeria anayankha chilimbikitso cha boma lake cha kuchepetsa chiŵerengero cha ana mwa kunena kuti: “Ndiri wotsirizira wa ana 26 a bambo wanga. Akulu anga onse, kuphatikizapo azichimwene ndi azichemwali, ali ndi ana oyambira pa asanu ndi atatu kufikira 12. Chotero kodi ine ndine amene ndiyenera kukhala ndi ana ocheperapo?”
Komabe, lingaliro lotero silofala monga momwe linaliri panthaŵi ina, ngakhale m’Nigeria, kumene mkazi wamba amabala ana asanu ndi mmodzi. Poyang’anizana ndi kukwera kwamitengo, mamiliyoni ambiri a anthu akuvutika kwambiri kudyetsa ndi kuveka mabanja awo. Ambiri aphunzira mwa kudziwonera okha chowonadi cha mwambi wa Ayoruba wakuti: “Ọmọ bẹẹrẹ, òṣì bẹẹrẹ” (kuchuluka kwa ana, ndiko kuchuluka kwa umphaŵi).
Okwatirana ambiri amazindikira mapindu a kulinganiza banja, komabe samakuchita. Kodi Chotulukapo nchiyani? The State of the World’s Children 1992, lofalitsidwa ndi United Nations Children’s Fund, linanena kuti pafupifupi mimba 1 mwa 3 m’maiko osatukuka mkati mwachaka sikokha kuti ikakhala yosalinganizidwa komanso yosafunika.
Kulinganiza Banja Kumapulumutsa Miyoyo
Kusiyapo mavuto azachuma, chifukwa chachikulu cholingalilira kulinganiza banja ndicho thanzi la nakubala ndi ana ake. “Kukhala ndi mimba nkosatsimikizirika ndipo kubala ndiko vuto la imfa ndi moyo.” umatero mwambi wa ku West Africa. Chaka chirichonse m’maiko osatukuka, akazi okwanira theka la miliyoni amafa ali ndi mimba kapena pobala, ana okwanira miliyoni imodzi amasiyidwa opanda mayi, ndipo mamiliyoni ena asanu kufikira ku mamiliyoni asanu ndi aŵiri a akazi amapundulidwa kapena kuvulazidwa ndi maupandu athanzi ophatikizapo kubala mwana.
Saali akazi onse m’maiko osatukuka amene amakhala ndi maupandu ofananawo. Monga momwe panopa bokosi likusonyezera, awo amene ali paupandu kopambana ndiwo akazi amene amabala ana ochulukitsitsa mofulumira kwambiri, mwakaŵirikaŵiri kwambiri, kapena mochedwa kwambiri. Akatswiri a UN akuyerekezera kuti kulinganiza banja kukapewetsa zoyambira pa mbali imodzi mwa zinayi kufikira ku mbali imodzi mwa zitatu ya imfazi ndipo kukapewetsa kupundulidwa kwa mamiliyoni ambiri.
Koma kodi kupulumutsa miyoyo mamiliyoni ambiri sikukanapindulitsa kokha kuwonjezereka kwa kukula kwa chiŵerengero cha anthu? Modabwitsa, akatswiri ambiri akunena kuti ayi. “Kungalingaliridwe kuti,” likufotokoza motero Human Development Report la 1991, “ngati ana owonjezereka anapulumuka, mavuto a chiŵerengero cha anthu akanaipirapo. Zosiyanazo ndizo zowona kwambiri. Kaŵirikaŵiri kubala kumachepa pamene makolo ali achidaliro mowonjezereka kuti ana awo adzapulumuka.”
Komabe, mamiliyoni ambiri a akazi, makamaka m’zitaganya zaumphaŵi, akupitirizabe kubala mwakaŵirikaŵiri. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti chitaganya chawo chikuwayembekezera kuti atero, chifukwa chakuti kukhala ndi ana ambiri kumawonjezera kuthekera kwakuti ena adzapulumuka, ndi chifukwa chakuti angakhale osadziŵa kapena osakhoza kupeza mautumiki a kulinganiza banja.
Komabe, akazi ambiri amene ali ndi mabanja aakulu sakanachitira mwina. Amalingalira mwana aliyense kukhala dalitso lochokera kwa Mulungu.
[Bokosi patsamba 28]
Mimba Zaupandu Kwambiri m’Maiko Osatukuka
Mofulumira Kwambiri: Upandu wa imfa mkati mwa kukhala ndi mimba ndi pobala mwana pakati pa akazi ausinkhu wazaka 15 kufikira 19 zakubadwa ngwaukulu kuŵirikiza katatu koposa akazi ausinkhu wazaka 20 kufikira 24 zakubadwa. Ana obadwa kwa akazi azaka 13-19 ali ndi kuthekera kwakukulu kwa kufa, kubadwa mofulumirirapo kwambiri, kapena kukhala aang’ono kwambiri pobadwa.
Motsatizana Pafupi Kwambiri: Utali wa nthaŵi ya pakati pa kubala ana otsatizana umayambukira kwambiri moyo wa mwana. Mwana wobadwa zaka zosafikira ziŵiri pambuyo poti mayi wabala wina ali ndi kuthekera kwa 66 peresenti kwa kufa adakali khanda. Ngati ana ameneŵa apulumuka, kukula kwawo mwachiwonekere kwambiri kuli kopinimbira ndipo kukula kwawo kwamaganizo mwachiwonekere kwambiri kuli kododometsedwa. Pafupifupi 1 mwa imfa za makanda 5 ikanapewedwa mwa kutanimphitsa koyenerera nthaŵi yobala. Kutanimphitsa kwa zaka zitatu kapena kuposerapo za kubala kuli ndi maupandu ochepa kwambiri.
Ochuluka Kwambiri: Kubala ana oposa anayi kumawonjezera masoka a kukhala ndi pakati ndi pobala mwana, makamaka ngati ana apapitawo sanasiyanitsidwe kwazaka zoposa ziŵiri. Pambuyo pa mimba zinayi, azimayiwo ali achiwonekere kwambiri kudzadwala nthenda yochepa mwazi ndipo ali ndi kuthekera kwambiri kwa kuchucha mwazi, ndipo ana awo amakhala paupandu waukulu wa kubadwa ali opunduka.
Mochedwa Kwambiri: Akazi azaka zoposa 35 zakubadwa ali ndi kuthekera kwa kufa kuŵirikiza nthaŵi 5 mkati mwa kukhala ndi pakati kapena pobala koposa akazi azaka zoyambira 20 kufikira 24 zakubadwa. Ana obadwa mwa akazi achikulirewo alinso ndi kuthekera kwambiri kwa kufa.
Magwero: World Health Organization, UN Children’s Fund, ndi UN Population Fund.