Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 10/8 tsamba 12-14
  • Kodi Ndani Ayenera Kusankha za Ukulu wa Banja?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndani Ayenera Kusankha za Ukulu wa Banja?
  • Galamukani!—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kulamulira Kubala—Nchifukwa Ninji Kuli Kochititsa Mkangano?
  • Zimene Baibulo Limanena
  • Pangani Zosankha Zimene Mungathe Kupirira Nazo
  • Njira Zopeŵera Kutenga Mimba—Kodi Ndani Ayenera Kusankha? Inu kapena Tchalitchi?
    Galamukani!—1989
  • Ana—Kodi Ndiwo Mapindu Kapena Mavuto?
    Galamukani!—1993
  • Kodi N’kulakwa Kugwiritsira Ntchito Njira za Kulera?
    Galamukani!—2007
  • Kulinganiza Banja—Lingaliro Lachikristu
    Galamukani!—1993
Onani Zambiri
Galamukani!—1996
g96 10/8 tsamba 12-14

Kodi Ndani Ayenera Kusankha za Ukulu wa Banja?

YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU BRAZIL

MWANA wamwamuna wamasiku atatu okha anasiyidwa m’thumba lapulasitiki pasteshoni ya sitima ya pansi pa nthaka. Koma nyuzipepala ina ya ku Brazil inanena kuti mabanja angapo anadzipereka kulera khandalo.

Ngakhale kuti zimenezo sizimachitikachitika, chiŵerengero cha ana osafunika ndi osiyidwa kuzungulira dziko lonse chikukula. Kaŵirikaŵiri ukholo wosamala umasoŵeka. Kodi kuletsa mimba ndiko njira yothetsera vutolo? Kodi kungakhale kulakwa kulinganiza ukulu wa banja lanu?

Malinga ndi World Health Organization, pafupifupi 50 peresenti ya mimba padziko lonse zimakhala zosazikonzekera. Kaŵirikaŵiri mimba simangokhala yosaikonzera komanso yosafunika.

Ambiri amafuna kupeŵa mimba, mwinamwake chifukwa cha thanzi, nyumba, kapena zothetsa nzeru kuntchito. Chifukwa chake, njira zoletsera mimba, monga mibulu yolamulira kubala kapena makondomu, nzofala. Kuchotsa mimba kapena kutseka chibereko kumagwiritsiridwanso ntchito monga njira zolamulira kubala. Ponena za kuchotsa mimba ku Brazil, nyuzipepala ya O Estado de S. Paulo ikuti: “World Health Organization ikuyerekezera kuti pachaka 5 miliyoni mwa akazi 13 miliyoni amene amatenga mimba m’Brazil amataya mimba mwamseri.” Ndiponso, magazini a Time ananena kuti 71 peresenti ya akazi a ku Brazil a msinkhu wobala ana amene amakhala ndi amuna amalamulira kubala. Mwa ameneŵa, 41 peresenti amagwiritsira ntchito mibulu ndipo 44 peresenti atseketsa chibereko.

Kufufuza kukusonyeza kuti 75 peresenti ya Abrazilu amaganiza kuti nkofunika kulinganiza chiŵerengero cha ana. Ena amakana kulinganiza banja chifukwa amakhulupirira choikidwiratu kapena chifukwa choganiza kuti chifuniro cha Mulungu nchakuti banja likhale ndi ‘ana ochuluka malinga ndi amene Mulungu amapatsa.’ Kodi ndani ayenera kusankha za ukulu wa banja—okwatiranawo kapena boma kapena chipembedzo?

Kulamulira Kubala—Nchifukwa Ninji Kuli Kochititsa Mkangano?

Ngakhale kuti chimalola rhythm method, Tchalitchi cha Roma Katolika, chipembedzo chachikulu koposa m’Brazil, chimaletsa njira zoletsera mimba, kaya zikhale za kuchotsa mimba kapena zina. Papa Paul VI anati: “Kugonana kulikonse kuyenera kulola moyo kupangika.” Papa John Paul II anati: “Kuletsa mimba, mutakulingalira mosamala, kuli kosaloledwa konse kwakuti sikungalungamitsidwe pachifukwa chilichonse.” Chotero, Akatolika ambiri amazengereza kulamulira kukula kwa mabanja awo, polingalira kuti kuletsa mimba ndi tchimo.

Komabe, magazini a zamankhwala a Lancet akuti: “Mamiliyoni adzakhala ndi moyo osaphunzira, ali paulova, osoŵa nyumba ndi osoŵa mautumiki ofunika koposa a zaumoyo, chithandizo cha boma ndi zaukhondo, ndipo kuwonjezereka kwa chiŵerengero cha anthu kosalamulirika ndiko chochititsa chachikulu.” Chifukwa chake, powopa kuchulukitsitsa kwa anthu ndi umphaŵi, maboma ena amalimbikitsa kulinganiza banja, ngakhale kuti tchalitchi chimatsutsa. Mwachitsanzo, “Costa Rica anatsitsa chiŵerengero choyenera cha ana [pabanja] kuchoka pa 7 kufika pa 3,” akutero katswiri wa biology Paul Ehrlich.

Chofalitsa cha United Nations, Facts for Life—A Communication Challenge chimati: “Mkazi atakhala ndi ana anayi, mimba zina zimadzetsa ngozi yaikulu pa moyo ndi thanzi la mayiyo ndi mwana yemwe. Makamaka ngati kubala kwapapitapo kunatsatizana zisanakwane zaka zoposa ziŵiri, thupi la mkazi lingafooke kwambiri chifukwa cha mimba zobwerezabwereza, kubala, kuyamwitsa, ndi kusamalira ana aang’ono.”

Mabanja aakulu akali ochuluka kumene imfa za ana zili zambiri, makamaka kumadera akumidzi a mu Afirika, Asia, ndi Latin America. Chifukwa ninji? Ambiri sadziŵa za njira zoletsera mimba. M’madera ena chochititsa china chingakhale chimene wopanga malamulo wina ananena kuti, “mwamuna amadziyesabe mwamuna weniweni kokha ngati mkazi wake akhala ndi mimba chaka chilichonse.” Jornal da Tarde ikutchula chimene chingakhalenso chochititsa china, makamaka malinga ndi kuganiza kwa akazi: “Ana ali zina za zinthu zosapezekapezeka zimene zimawapatsa chimwemwe ndi chikhutiro chaumwini.” Ndiponso, Paulo Nogueira Neto, amene kale anali mlembi wa bungwe la malo okhala m’Brazil, anati: “Mwana ndiye chuma chamtsogolo cha anthu osauka.”

Zimene Baibulo Limanena

Kodi mukudziŵa kuti Mawu a Mulungu, Baibulo, amasiyira mwamuna ndi mkazi wake kuti asankhe za ukulu wa banja? Amasonyezanso kuti ukwati ngwoyenera monga njira yobalira ana kapena yosonyezera chikondi mwa kugonana kolemekezeka.—1 Akorinto 7:3-5; Ahebri 13:4.

Koma kodi Mulungu sanauze Adamu ndi Hava m’Paradaiso ‘kubalana, kuchuluka, kudzaza dziko lapansi’? (Genesis 1:28) Inde, komabe palibe chilichonse m’Baibulo chimene chimasonyeza kuti ife tili pansi pa lamulo limodzimodzilo lerolino. Mlembi Ricardo Lezcano ananena kuti: “Zikuoneka kukhala zowombana kugwiritsira ntchito pa anthu [mabiliyoni ambiri] malangizo amodzimodziwo amene anaperekedwa kwa anthu aŵiri okha okhala pa pulanetili.” Ngakhale ngati anthu asankha kusakhala ndi ana konse, chimenechi ndi chosankha chawo choyenera kulemekezedwa.

Chokondweretsa nchakuti New Catholic Encyclopedia imanena kuti lingaliro la Mboni za Yehova lili la m’Baibulo. Imati: “Kusiyapo kulamulira kubala, kumene amasiyira okwatirana kuti adzisankhire, makhalidwe awo a muukwati ndi a kugonana ngamphamvu kwambiri.” Imawonjezera kuti: “Iwo amaona Baibulo kukhala magwero awo okha a chikhulupiriro ndi miyezo ya khalidwe.”

Kodi njira zonse zochepetsera ukulu wa banja nzoyenera? Ayi. Popeza kuti moyo ngwopatulika, Chilamulo cha Mulungu kwa Israyeli chinati aliyense amene anachotsetsa mimba anayenera kuonedwa monga wambanda. (Eksodo 20:13; 21:22, 23) Ponena za kuletsa kubala, konga kuja kochitidwa mwa vasectomy (kudula mtsempha wa ubwamuna), chosankha chimadalira pa chikumbumtima cha munthu mwini, pakuti zimenezi sizimatchulidwa molunjika m’Baibulo. “Yense adzasenza katundu wake wa iye mwini.” (Agalatiya 6:5)a Ndipo popeza kuti pali njira zosiyanasiyana zolamulirira kubala, malangizo a madokotola angathandize okwatirana kusankha ngati akufuna kugwiritsira ntchito njira ina kapena sakufuna.

Pangani Zosankha Zimene Mungathe Kupirira Nazo

Simungalinganize zinthu zonse m’moyo. Koma kodi mungagule galimoto kapena nyumba popanda kulingalirapo kwambiri pa zofunika zake? Galimoto kapena nyumba ingagulitsidwenso, koma ana ngosabwezeka. Choncho, pokonzekera mimba kodi kukhoza kwa mwamuna ndi mkazi kusamalira zofunika za moyo sikuyenera kulingaliridwa?

Ndithudi, sitingafune kuti banja lathu likhale losadya bwino, ndiponso sitingafune kukhala mtolo kwa ena. (1 Timoteo 5:8) Panthaŵi imodzimodziyo, kuwonjezera pa chakudya ndi nyumba, ana amafunikira maphunziro, mwambo, ndi chikondi.

Kuwonjezera pa kuŵerengera zofunika zonga ntchito, ndalama, ndi kuleza mtima, thanzi la mkazi liyeneranso kulingaliridwa. Kulinganiza mwanzeru nthaŵi ya kukhala ndi mimba kumapulumutsa moyo ndi kuchirikiza thanzi labwino. Facts for Life imati: “Imodzi ya njira zabwino koposa zochepetsera ngozi za mimba ndi za kubala mwana kwa mayi ndi mwana yemwe ndiyo kulinganiza bwino nthaŵi ya kubala. Pamakhala ngozi yaikulu pa kubala mwana pamene wodzakhala mayiyo ali ndi zaka zosakwanira 18 kapena zoposa 35, kapena ngati anakhalapo ndi mimba zinayi kapena kuposapo kumbuyoku, kapena ngati pali mpata wa zaka zosakwanira ziŵiri kuchokera pa kubala kwapapitapo.”

Okwatirana omwe akuganiza zokhala ndi ana ayenera kukumbukira kuti, malinga ndi ulosi wa Baibulo, tazingidwa ndi dziko lodzala ndi upandu, njala, nkhondo, ndi kusatsimikizirika kwa chuma. (Mateyu 24:3-12; 2 Timoteo 3:1-5, 13; Chivumbulutso 6:5, 6) Chikondi chenicheni pa ana chidzathandiza okwatirana kukhala oona mtima ponena za dziko limene tikukhalamo, akumazindikira kuti kulera ana nthaŵi ino nkovuta kwambiri. Chotero m’malo mwa kungolekerera zinthu kumachitika ndi kukhala ndi ana ambirimbiri kosalamulirika akumayembekezera kuti zonse zidzakhala bwino, ambiri amasankha ukulu wa banja lawo kuti ana awo adzapeze chimwemwe chachikulu ndi chisungiko.

Kuwonjezera pa kutithandiza kusankha mwanzeru pa nkhani zabanja, Mawu a Mulungu amatipatsa chiyembekezo cholimba cha mtsogolo. Baibulo limasonyeza kuti chifuno cha Mlengi nchakuti anthu akhale kosatha mumtendere ndi chimwemwe padziko lapansi la paradaiso. Kuti achite zimenezi, Mulungu posachedwapa adzathetsa dongosolo loipali la zinthu. Ndiyeno, m’dziko latsopano lolungama lopanda umphaŵi ndi kuchulukitsitsa kwa anthu, ana sadzatayidwanso chifukwa chosafunika.—Yesaya 45:18; 65:17, 20-25; Mateyu 6:9, 10.

Ndithudi, kulingalirana ndi kulingalira ana, limodzi ndi lingaliro loyenera la kubala, zidzathandiza okwatirana kusankha za ukulu wa banja lawo. M’malo mwa kungolekerera zinthu kuchitika mosalamulirika, iwo ayenera mwapemphero kufunafuna chitsogozo cha Mulungu. “Madalitso a Yehova alemeretsa, sawonjezerapo chisoni.”—Miyambo 10:22.

[Mawu a M’munsi]

a Onani Nsanja ya Olonda yachingelezi ya May 1, 1985, tsamba 31.

[Chithunzi patsamba 12]

Ana mamiliyoni ambiri amasiyidwa

[Chithunzi patsamba 14]

Ana amafuna chisamaliro chachikondi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena