Kukula kwa Chiŵerengero cha Anthu Chapadziko Lonse—Nkhani Yaikulu
“MWANA Wofikitsa Chiŵerengero cha Mabiliyoni Asanu.” Ndimo mmene boma la China linatchulira Wang He, mwana wamtsikana wobadwira m’chipatala cha Beijing pakati pausiku, July 11, 1987. Kuti mwana ameneyo anafikitsadi chiwonkhetso cha chiŵerengero chapadziko lonse lapansi cha anthu 5,000,000,000 panthaŵiyo kapena ayi, palibe aliyense adziŵa. Mosasamala kanthu za zimenezo, iye anabadwa panthaŵi yeniyeni yosonyezedwa ndi Mitundu Yogwirizana kukhala pamene chiŵerengero cha anthu chapadziko lonse kukafikira chiŵerengero chimenecho. Boma la China linangogwiritsira ntchito chochitikacho kokha kufalitsira nkhani yaikulu ya kukula kwa chiŵerengero cha anthu yoyang’anizana ndi China ndi dziko lonse.
Ziŵerengero zikusonyeza kuti chiŵerengero cha anthu padziko lapansi chikuwonjezereka pamlingo umene ukuwopsa akatswiri ena. Pamlingo watsopano wa kukulako, chiŵerengero chapadziko lapansi chidzaŵirikiza kaŵiri mkati mwazaka pafupifupi 40 zokha. Akatswiri akutiuza kuti, pamlingo umenewo, kuchuluka kwachakudya chofunika kudyetsa chiŵerengero chapadziko lonse mwamsanga chidzachuluka koposa chotulutsidwa, ndipo chotulukapo chidzakhala njala ya padziko lonse. Ndiponso, popeza kuti chakudya chimene dziko limatulutsa chiri ndi polekezera, chimenechi chidzatha mwamsanga kwambiri ndi kukula kwa chiŵerengero cha anthu, ndipo zimenezo zingatanthauze kokha chipoloŵe chapadziko lonse lapansi. Akatswiri akunena kuti, ngati kusoŵeka kwachakudya ndi zinthu zina sikukupangitsa chiwonongeko chathu, kuwononga malo otizungulira kumene tikuchita mosakaikira kudzatero. Ife kwenikweni tikudzivulaza ndi zimene tikuchitira mpweya, madzi, ndi nthaka, ndipo anthu owonjezereka adzangokulitsa kokha mlingowo. Zonsezi zikumvekera kukhala kudza kwa tsoka.
Komabe, kodi nchiyani chimene chingachitidwe ndi nkhaniyi? Pali malingaliro ambiri onena za nkhaniyo. Ena akulingalira kuti kusiyapo ngati kachitidwe kotsimikiza kakutengedwa kuchepetsa kukula kwa chiŵerengero cha anthu, mkhalidwe wa anthu onse udzaikidwa pachiswe. Ena amakhulupirira kuti monga momwe zinaliri m’nthaŵi yapitayo, njira zatsopano zidzapezedwa zochitira ndi mavuto a chakudya, nthaka, kuipitsidwa kwa zinthu, ndi zirizonse zimene zikuphatikizidwa. Enabe akulingalira kuti chiwonkhetso cha chiŵerengero cha anthu potsirizira pake chidzakhala cholingana, chotero palibe kufunika kochiderera nkhaŵa kwambiri. Kunena zowona, pali malingaliro amphamvu ndi maganizo ponena za pafupifupi mbali iriyonse yankhaniyo. Mwachiwonekere, kukula kwa chiŵerengero cha anthu chapadziko lonse ndinkhani yodzutsa mkangano ndi yaikulu.
Komabe, choyenera kulingaliridwa nchakuti anthu okhala m’maiko amene ali omwazikana ndi olemera mwapang’ono kaŵirikaŵiri ndiwo amene amalankhula mwamphamvu kwambiri za kudza kwa chiwonongekocho. Iwo amalankhula za mantha awo chifukwa chakuti amawona kuti mlingo wa kakhalidwe kawo kapena mkhalidwe wawo wamtsogolo ukuwopsezedwa. Koma bwanji za awo amene akukhala m’maiko osauka, osatukuka, kapena ochulukiridwa ndi anthu? Kodi iwo amalingalira motani za nkhani ya kuchuluka kwa anthu? Kodi moyo ngwotani m’ngodya zadziko mmene anthu ali ochulukitsitsa?
Galamukani! akukutengerani ku ena a malo okhalidwa ndi anthu ochulukitsitsa adziko kukupatsani lingaliro lenileni la mmene kuliri kukhala ndi moyo pansi pa chitsenderezo cha kuchulukitsitsa kwa anthu ndi kukuthandizani kumvetsetsa zina za nkhani zophatikizidwa.