Tsamba 2
Kuwonjezereka Kwakukulu kwa Anthu—Kodi Kumawopseza Mtsogolo Mwathu? 3-14
“Kuwonjezereka kwakukulu kwa anthu,” “ngozi ya kuchuluka kwa anthu,” “kupanikiza kwa chiphunzitso cha Malthus”—ameneŵa ndiochepa chabe a mawu ogwiritsiridwa ntchito kufotokoza chiwopsezo cha mkhalidwe wa moyo wamtsogolo. Koma kodi bwanji ponena za tsopano lino? Kodi kuwonjezereka kwakukulu kwa anthu kungakuyambukireni motani? Kodi ndimotani mmene kuliri kukhala ndi moyo m’mizinda mmene anthu amakhala mopanikizana kwambiri? Ndipo bwanji ponena za mtsogolo? Mpambo uno wa nkhani ukupenda mafunso ameneŵa.
Kodi Kutchova Juga Kulidi Koipa Kwambiri? 19
Ambiri amamwerekera ndi kutchova juga adakali achichepere. Kodi kungatsogolere kuchiyani? Kodi nchifukwa ninji muyenera kukaniza chisonkhezerocho?