Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g93 4/8 tsamba 32
  • Aphunzitsi Apatsa Mpata Chilengedwe

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Aphunzitsi Apatsa Mpata Chilengedwe
  • Galamukani!—1993
Galamukani!—1993
g93 4/8 tsamba 32

Aphunzitsi Apatsa Mpata Chilengedwe

Sukulu ina m’Berlin, Jeremani, inaika chithunzithunzi pa chipupa chachikulu chosonyeza mmene zolengedwa zonga anyani zinasinthira kukhala anthu amakono, malinga nzimene ena amakhulupirira. Tsiku lina, ophunzira atafika pasukulu anapeza kuti chithunzithunzicho chinafafanizidwa ndi utoto woyera. Kodi chinachitika nchiyani?

Wophunzira wina wazaka 16 wotchedwa Natalie, mmodzi wa Mboni za Yehova, anafunsa mphunzitsi wake wa sayansi ya biology chifukwa chake chithunzithunzicho chinafafanizidwa. Mphunzitsiyo anafotokoza kuti wophunzira wina adampatsa buku la Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? Bukulo linamkondweretsa kwambiri kwakuti anakalisonyeza kwa aphunzitsi anzake ophunzitsa biology. Bukulo linawachititsa chidwi nawonso.

Chotero, aphunzitsiwo anapanga chosankha chakuti afafanize chifanizirocho kuwopera kuti, malinga ndi kunena kwawo, ‘asayambirire kupotoza malingaliro a ophunzirawo.’ Chotero m’malo mwakuphunzitsa ophunzirawo nthanthi yokha ya chisinthiko, aphunzitsiwo analinganizanso kuphunzitsa za chilengedwe, mwakugwiritsira ntchito nkhani za mu Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation?

Buku lokongola limeneli limafalitsidwa ndi Mboni za Yehova, gulu la padziko lonse la ophunzira Baibulo oposa pa mamiliyoni anayi odzipereka kuthandiza anthu kuphunzira zowonjezereka ponena za zifuniro za Mlungu. Ngati mungakonde kudziŵa zowonjezereka kapena phunziro la Baibulo lapanyumba laulere, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 33459, Lusaka 10101, kapena ku keyala yoyenera pa ondandalitsidwa patsamba 5.

[Chithunzi patsamba 32]

Life—How did it get here? By evolution or by creation?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena