Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g93 8/8 tsamba 20
  • Mliri wa Kupsinjika Maganizo kwa Ana

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mliri wa Kupsinjika Maganizo kwa Ana
  • Galamukani!—1993
  • Nkhani Yofanana
  • Makolo Anga Akulekana—Kodi Ndichitenji?
    Galamukani!—1990
  • Zimene Zimachititsa Moyo Kukhala Wopanikizika ndi Zotsatirapo Zake
    Galamukani!—2005
  • Kupanikizika Maganizo Kwabwino ndi Koipa
    Galamukani!—1998
  • Zimene Tingachite Kuti Tisamapanikizike Kwambiri
    Galamukani!—2010
Onani Zambiri
Galamukani!—1993
g93 8/8 tsamba 20

Mliri wa Kupsinjika Maganizo kwa Ana

“RANDY!” Anakuwa motero Rita, atachita mantha ndi zimene anaona ali patali pamene anali kufika panyumba pake. Anaona mwana wake wamwamuna Randy, atatulutsa kale thupi lonse kufikira m’chuuno pazenera la m’chipinda chake chogona, ali pautali wa mamita asanu ndi atatu pamwamba ndipo pansi pakepo pali konkili. M’nyumbamo, Larry anamva kukuwa kochititsa mantha kwa mkazi wake ndipo anathamangirako. Akukwera m’chipinda chapamwambacho mwaliŵiro, anakagwira Randy, namkokera mkatimo. Makolo a Randy anafuna mayankho ofulumira. “Kodi nchifukwa ninji wachita zimenezo? Nchifukwa ninji?” iwo anafunsa mosakhulupirira zimene zanachitika. “Ukanavulala; ukanafa!” “Ndinafuna kuti ndife,” anayankha motero Randy mosasalama kanthu. Randy anali wa zaka zisanu chabe.

MWA maonekedwe onse akunja, Randy anali mnyamata wabwino ndi wathanzi. Palibe aliyense amene anaganizira zakuti mumtima mwake iye anafuna kuti afe. Komabe, mauphungu operekedwa pambuyo pake anavumbula kuti Randy anali mwana wopsinjika maganizo kwambiri.

Mofanana ndi Randy, ana osaŵerengeka lerolino akukanthidwa ndi kupsinjika maganizo kwakukulu. Polephera kupeza njira zabwino zothetsera kupsinjika kwawoko, ena mosaphula kanthu amayesa kupondereza nkhaŵa zawozo. Koma kupsinjika kotsekerezedwa mkati m’kupita kwanthaŵi kumapezabe potulukira. Kwa ena, nkhaŵa imene siitulutsidwa mwa kuilankhula kwa ena imachititsa matenda kapena mkhalidwe wopulupudza. Kwa enanso, nkhaŵa yotsekeredwa mkati imachititsa machitachita odziwononga, kuphatikizapo kudzivulaza dala, mavuto akadyedwe, kugwiritsira ntchito molakwa zoledzeretsa, ndipo ngakhale kudzipha ndithu. Buku lakuti The Child in Crisis limanena kuti: “Ambiri a mavuto ameneŵa—makamaka kudzipha—m’nthaŵi zakumbuyo analingaliridwa kukhala ochitika kwa achikulire okha ndi achichepere. Tsopano akuonekera kukhala akuyambukiranso ana aang’ono.”

‘Kodi zimenezi zingachitike motani?’ amafunsa motero achikulire odandaula. ‘Kodi ubwana sindiyo nthaŵi ya kumangoseŵera ndi zidole ndi kuchita maseŵera, nthaŵi ya kuchita zoseketsa ndi zosangalatsa?’ Kwa ana ambiri yankho nlakuti ayi. “Kunena kuti ubwana uli nthaŵi ya kusangalala kokhakokha kuli malingaliro ongopekedwa ndi achikulire,” akutero Dr. Julius Segal. Chenicheni chimenechi chatsimikiziridwa ndi wochiritsa ana Joseph Lupo kuti: “Ndagwira ntchito yakuchiritsa kwa zaka makumi aŵiri ndi zisanu tsopano. Lerolino ndimasamalira unyinji woŵirikizika kanayi wa ana aang’ono ndi achinyamata opsinjika maganizo.”

Kodi nchiyani chimene chimachititsa kupsinjika maganizo koposa ndi kalelonse koteroko mwa ana? Kodi pamakhala zizindikiro zochenjeza zotani? Kodi ana opsinjika maganizo angathandizidwe motani? Mafunsoŵa adzayankhidwa m’nkhani zotsatira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena