Tsamba 2
Kodi Ndani Adzatetezera Nyama Zathu za Kuthengo? 3-11
Kuwonongedwa kwa nyama za kuthengo mu Afrika kuli mkhalidwe weniweni umene umapezeka mbali zina za dziko. Umbombo ndi kukhulupirira malaulo zili zinthu ziŵiri zimene zimachirikiza kuphedwa kwa nyama kosafunika. Kodi ndani amene kwenikweni amasamala?
Monga Wothaŵa, Ndinapeza Chiweruzo Cholungamadi 12
Nkhani yochititsa chisoni ya Mgiriki wobadwira ku Palestine amene anamenya nkhondo kuti apeze moyo watsopano m’dziko lachilendo kwambiri.