Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g93 12/8 tsamba 26-28
  • Kodi Ndani Akhoza Kundithandiza Kuthetsa Mavuto Anga?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndani Akhoza Kundithandiza Kuthetsa Mavuto Anga?
  • Galamukani!—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ausinkhu Wanu—Kodi Angapereke Uphungu Wabwino Koposa?
  • Phindu la Kukhala ndi Makolo Owopa Mulungu
  • ‘Samandimvetsetsa!’
  • Pezani Nokha Nzeru Yogwira Ntchito!
  • Kodi Ndiyenera Kufotokozera Munthu Wina Kuti Ndikuvutika Maganizo?
    Galamukani!—2000
  • Kodi Ndingatani Kuti Ndidziwane Bwino Ndi Makolo Anga?
    Galamukani!—2009
  • Kodi Achinyamata Angapeze Bwanji Thandizo?
    Galamukani!—2009
  • Kodi Ndingatani Makolo Anga Akamakangana?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
Onani Zambiri
Galamukani!—1993
g93 12/8 tsamba 26-28

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ndani Akhoza Kundithandiza Kuthetsa Mavuto Anga?

“MUNTHU abadwira mavuto.” Anatero munthu wina wopsinjika maganizo wotchedwa Yobu pafupifupi zaka zikwi zinayi zapitazo. (Yobu 5:7) Mwinamwake moyo wanu suli watsoka kwambiri mofanana ndi wa Yobu. Koma mosakayikira inunso mwakhala ndi gawo lanu la mavuto ndi zopweteka.

Pamene gulu lina la achichepere a ku America linafunsidwa kuti, “Kodi nchiyani chimakuvutitsani maganizo kwambiri?” ambiri anatchula sukulu, makolo, ndalama, mabwenzi, ndi abale awo kukhala magwero a nkhaŵa zawo. Bwanji za inuyo? Kodi mukuyang’anizana ndi chitsenderezo cha ausinkhu wanu, nkhaŵa za ndalama, kapena mavuto a kusukulu? Kodi kumakukhalirani kovuta kuchita ndi mavuto akuthupi ndi amaganizo a unamwali? Kodi muli odera nkhaŵa ndi mtsogolo mwanu?

Ndi mavuto onseŵa m’maganizo mwanu, nkwapafupi kupsinjika mtima ndi kuchita tondovi. Kwenikweni, ngati mungosunga mumtima nkhaŵa zoterozo, mungaone kuti mukudzilekanitsa ndi ena mwamaganizo. (Yerekezerani ndi Miyambo 18:1.) Pamenepo, kodi muyenera kuchita motani kuti muthetse mavuto anu? Kodi muyeneradi kulimbana nawo panokha?

Iyayi, chifukwa chakuti mavuto anu—chinkana kuti angaoneke kukhala aakulu—sali achilendo. Atapenda mosamalitsa mkhalidwe wa anthu, mfumu yanzeru Solomo anati “palibe kanthu katsopano pansi pano.” (Mlaliki 1:9) Inde, ena ayang’anizana ndi kuthetsa mwachipambano mavuto ofanana ndi anu. Chotero simufunikira nthaŵi zonse kulimbana ndi mavuto panokha; nthaŵi zina mungapeze chithandizo kwa munthu wina amene anayang’anizanapo kale ndi zimenezo. Ndi iko komwe, ngati munali kupita kumalo achilendo, kodi simungafune kufunsira kayendedwe kwa munthu wina amene anapitako kale kumeneko? Funso nlakuti, Kodi chithandizo choterocho mungachifune kwa yani?

Ausinkhu Wanu—Kodi Angapereke Uphungu Wabwino Koposa?

Achichepere ambiri amafuna kukambitsirana mavuto awo ndi ausinkhu wawo. “Nthaŵi zina ndimaganiza kuti masinthidwe ena amene akuchitika kwa ine ali achilendo,” akufotokoza motero wachichepere Anita. “Ndimalingalira kuti, ‘Kodi zimenezi zimachitika kwa wina aliyense?’ Ndimadzifunsa ndekha ngati kuli kupusa kwa ine kumalingalira motero.” Mungalingalire kuti wina wake wausinkhu wanu angamvetsetse malingaliro anu ndi kuti munthu wachikulire—makamaka kholo—angakhale olingalira moweruza, kapena osuliza monkitsa.

Koma pamene kuli kwakuti ausinkhu wanu angamvetsetse mkhalidwe wanu, ndi kuchita chifundo, sinthaŵi zonse pamene angapereke uphungu wabwino kwambiri. Monga momwe Baibulo limafotokozera, “anthu akulu msinkhu . . . ali ndi mphamvu za kulingalira zophunzitsidwa kusiyanitsa chabwino ndi choipa.” Motani? Baibulo limayankha kuti: “Mwa kugwiritsira ntchito kwanthaŵi yaitali,” ndiko kuti, chidziŵitso! (Ahebri 5:14; The New English Bible) Pokhala opanda chidziŵitso choterocho, achichepere sanakulitse kwenikweni “nzeru yeniyeni ndi kulingalira” kofikira pamlingo wa munthu wachikulire. (Miyambo 3:21) Chifukwa chake, kulabadira uphungu wa wachichepere mnzanu kuli kwangozi. Lemba la Miyambo 11:14 limachenjeza kuti: “Popanda upo wanzeru anthu amagwa.”

Phindu la Kukhala ndi Makolo Owopa Mulungu

Kaŵirikaŵiri achikulire amakhala pamalo abwino akupereka chilangizo chaluso. Yobu wolungamayo ananena mwanjira iyi: “Kwa okalamba kuli nzeru, ndi kwa a masiku ochuluka luntha.” (Yobu 12:12) Mwachionekere, amene ali oyenera koposa kukuthandizani pambali imeneyi ndiwo makolo anu owopa Mulungu. Choyamba, iwo amakudziŵani bwino kuposa munthu wina aliyense. Pokhala kuti anakumana ndi ina ya mikhalidwe imene mukuyang’anizana nayo tsopano, iwo akhoza kukuthandizani kwambiri kukupeŵetsani mavuto. Polankhula monga kholo, Solomo analangiza kuti: “Ananu, mverani mwambo wa atate, nimutchere makutu mukadziŵe luntha; pakuti ndikuphunzitsani zabwino.”—Miyambo 4:1, 2.

Talingalirani za mwamuna wachichepere wa ku Ghana wotchedwa Samuel. Pamene anali ku sukulu ya sekondale, anafunikira kusankha kaya kulondola maphunziro akudziko kapena ntchito yodzisankhira monga mtumiki wanthaŵi yonse wa Mboni za Yehova. “Popeza kuti banja lathu linali logwirizana kwambiri ndi kulankhulana kwabwino,” iye akutero, “kunali kosavuta kuululira makolo anga.” Makolo a Samuel anamsonkhezera m’njira ya utumiki wanthaŵi yonse—ntchito imene akupitabe nayo patsogolo. Samuel akuvomereza kuti achichepere akhale akumaloŵetsamo makolo awo poyesa kuthetsa mavuto awo chifukwa chakuti “iwo ali ndi chidziŵitso chokulirapo m’moyo ndipo angakhale anakumanapo ndi mavuto amodzimodziwo . . . ndipo ali pamalo abwino akupereka lingaliro lawo lomvekera bwino pambali zonse za nkhaniyo.”

Mokondweretsa, malinga ndi kufufuza kwaposachedwapa kochitidwa ku Gallup, chiŵerengero chachikulu cha achichepere amafuna chitsogozo cha makolo—ngakhale pankhani zonga anamgoneka, sukulu, ndi za kugonana.

‘Samandimvetsetsa!’

Komabe, mwachisoni, achichepere ambiri amadzilekanitsa kwa makolo awo pamene aloŵa m’zaka za 13 mpaka 19. Ena amalingalira monga momwe anachitira mnyamata wina amene anati: “Ndayesa kulankhula kwa makolo anga ponena za mmene ndimaopera magiredi ndi kuti maphunzirowa ngondiumira kwambiri, koma amangondiuza kuti ndine waulesi ndipo ndiyenera kuŵerenga kwambiri.” Mtsikana Wachikristu wina mu Afrika anasonyeza nkhaŵa yofananayo, akumati: “Mkati mwanga, ndikudziŵa kuti ndili ndi mavuto anga amene ndifunikira thandizo, koma ndikuopa kuti makolo anga sadzamvetsetsa.”

Ndithudi, ngakhale makolo owopa Mulungu nthaŵi zina amaphophonya. Iwo angachite mopambanitsa pazinthu zina, angalephere kumvetsera, angakumveni molakwa, kapena kukhala olingalira moweruza. Komabe, izi sizitanthauza kuti muyenera kuwanyalanyaza m’moyo wanu. Yesu Kristu analeredwa ndi makolo opanda ungwiro. Komabe, Baibulo limasonyeza kuti Yesu anapitirizabe ‘kuwamvera iwo.’ Mosakayikira, chisonkhezero chawo chinamthandiza ‘kukulabe m’nzeru . . . ndi m’chisomo cha pa Mulungu ndi cha pa anthu.’—Luka 2:51, 52.

Kodi inu mumapindula ndi nzeru ya makolo anu ndi chidziŵitso chawo? Ngati simutero, talingalirani zimene zanenedwa m’buku lakuti Adolescence, lolembedwa ndi Eastwood Atwater kuti: “Pamene [azaka za 13 mpaka 19] asonkhezeredwa mosayenera ndi ausinkhu wawo, mwachionekere kumakhala chifukwa cha kanthu kena kosoŵeka muunansi wa makolo ndi achichepere osati chifukwa cha chikoka cha unansi wa ausinkhu wawo.” Kodi muli ndi unansi wa mtundu wanji ndi makolo anu? (Agalatiya 6:5) Kodi kungakhale kuti mwakhala mukupeŵa kulankhulana nawo posachedwapa? Pamenepo bwanji osachita zimene mungathe kuwongolera zinthu?a Zimenezi zili mbali ya zimene Solomo anatcha kukhala ‘mwana wokondedwa’ wa makolo a munthuwe.—Miyambo 4:3.

Malcolm, wachichepere wa ku Ghana amene tsopano akukhala ku United States, panthaŵi ina analingalira kuti makolo ake sanamvetsetse malingaliro ake. Koma iwo anaumirira pakumphunzitsa chidziŵitso cha m’moyo wawo ndi chilangizo cha Mawu a Mulungu. M’kalata yake yaposachedwapa kwa makolo ake, Malcolm analemba kuti: “Ndidziŵa kuti tinakhala ndi mikangano m’nthaŵi yapitayo. Koma ndikalingalira za masikuwo, ndimachita chidwi ndi njira imene munapiririra kuuma khosi kwanga ndi kuvomereza zina za zosankha zimene ndinazipanga. Kunena zowona, ndikudziŵa zimene zimachitika m’nyumba zina, ndipo Baibulo linathandizadi [m’nyumba yathu.] Ndibwerezanso, zikomo kwambiri.”

Pezani Nokha Nzeru Yogwira Ntchito!

Mmalo mwa kudodometsa kukula kwanu, kulandira chitsogozo cha makolo anu kungakhale njira yapafupi yofikira uchikulire. M’kupita kwanthaŵi nanunso mungakulitse ‘kuchenjera, chidziŵitso, ndi luso la kulingalira.’ (Miyambo 1:4) Mudzakhala wokonzekeretsedwa kupenda mavuto ndi kupeza malingaliro olama owathetsera.

Ndithudi, siachichepere onse amene ali ndi dalitso la kukhala ndi makolo owopa Mulungu. Komabe, kukakhala kulakwa kuganiza kuti simuyenera kusamalira kwambiri zimene makolo anu amanena kokha chifukwa chakuti sali Akristu. Iwo ndimakolo anu ndithu, ndipo ayenera kulemekezedwa pachifukwa chimenecho. (Aefeso 6:1-3) Ndiponso, ngati muwapatsa mpata, mungapeze kuti ali ndi zambiri zokuthandizani nazo monga uphungu wogwira ntchito. Pamene mufunikira chitsogozo chauzimu, yesani kuululira chiŵalo chodalirika cha mpingo Wachikristu. Kumeneko, sikuyenera kukhala kovuta kupeza wachikulire wowopa Mulungu amene adzamvetsera mowona mtima, ndi mtima womvetsetsa ndi wachifundo.

Kumbukiraninso kuti, mzimu wa Yehova uli mphamvu yokonzekeretsedwa nthaŵi zonse kuthandiza ndi kulimbitsa awo oufunafuna. (Luka 11:13) Yehova wagaŵiranso chuma cha chidziŵitso chimene chilipo kaamba ka inu m’Baibulo ndi zofalitsidwa zozikidwa pa Baibulo za Watch Tower Society. Eya, ngakhale mpambo wa nkhani unowu wathandiza zikwizikwi za achichepere kupeza mayankho othandiza pamavuto awo! Mwakuphunzira kupenda ndi kufufuza, mungakhale wokhoza kuthetsa mavuto ambiri panokha.—Miyambo 2:4.

Ndithudi, kuyang’anizana ndi mavuto kuli mbali ya moyo. Koma kumathandiza kukhala ndi lingaliro labwino limene wamasalmo anali nalo. Iye analemba kuti: “Kundikomera kuti ndinazunzidwa; kuti ndiphunzire malemba anu.” (Salmo 119:71) Inde, kuthetsa mavuto kungakuumbeni ndi kukuphunzitsani. Koma simuyenera kulimbana nawo panokha. Pezani chithandizo. Kaŵirikaŵiri chimakhalapo kwa ochipempha.

[Mawu a M’munsi]

a Kuti mupeze malingaliro angapo othandiza pankhani imeneyi, onani mutu 2 wa buku lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Chithunzi patsamba 26]

Kulandira chitsogozo cha makolo kungakhale njira yapafupi yofikira uchikulire

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena