Linachepetsa Kwambiri Uchiwerewere
Phungu wina payunivesite ya mu Oklahoma, U.S.A., anasimba kuti buku lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza lachita zotchulidwa pamwambapa. Phunguyo pa Langston University analemba kuti:
“Ndikulangiza munthu aliyense amene akuchita ndi achichepere a misinkhu ya pakati pa 13-18 kugwiritsira ntchito bukulo. Limalongosola zakugonana m’njira zimene ophunzira athu ayenera kudziŵa kotero kuti achite ndi mavuto a chitaganya chamakono chovutachi. Ponena za chokumana nacho changa, ndinapeza kuti limawathandiza kudziŵa zimene zimachitika ngati akhala auchiŵereŵere. Limawadziŵitsa za matenda osiyanasiyana opatsirana mwa kugonana monga ngati AIDS, chinzonono, zilonda za kumpheto ndi chindoko.
“Ngati musankha kugonana, limasonyeza mmene muyenera kusankhira wogonana naye mmodzi yekha kwa moyo wonse, ndipo limachirikiza chiyero cha ukwati. Ndasangalala kwambiri kugwiritsira ntchito buku limeneli. Lili ndi chiyambukiro pa miyoyo ya amene aligwiritsira ntchito. Ndinaona kuti chiŵerengero cha atsikana m’programu yathu otenga mimba chinatsika kwambiri pamene linasonyezedwa.”
Ngati mungakonde kulandira kope la buku lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza kapena kukhala ndi phunziro la Baibulo lapanyumba laulere, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 33459, Lusaka 10101, kapena ku keyala yoyenera patsamba 5.