Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 3/8 tsamba 31
  • Njovu—Mabwenzi Kapena Adani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Njovu—Mabwenzi Kapena Adani?
  • Galamukani!—1994
  • Nkhani Yofanana
  • Ulendo Wokaona Malo ku Ghana
    Galamukani!—2001
  • Chinenero cha Kutchire—Kulankhulana Kodabwitsa kwa Zinyama
    Galamukani!—2002
  • Tsaganani Nafe Paulendo Wathu wa Pamtsinje wa Chobe
    Galamukani!—1990
  • Zimatheka Bwanji Kuphunzitsa Njovu?
    Galamukani!—2009
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 3/8 tsamba 31

Njovu—Mabwenzi Kapena Adani?

NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU SOUTH AFRICA

NJOVU zimaonedwa kukhala zamtengo wapatali pazifukwa zosiyanasiyana ndipo zimadedwa pazifukwa zina. Kwa ena zili antchito amtengo wapatali, akatswiri okoka zipinjiri zazikulu ndi kuziika m’mizera yabwinobwino. Ena amaona njovu kukhala zamtengo wapatali chifukwa cha minyanga, zikopa, ndi nyama yake. Ena amangoziona monga zowononga minda ndi dzinthu dzawo.

Komabe, ofufuza ambiri amaona njovu kukhala zamtengo wapatali chifukwa cha njira zawo zosangulutsa. Cynthia Moss anathera zaka 13 akuphunzira makhalidwe a njovu m’nkhalango yosungira zinyama ya Amboseli ya ku Kenya. M’buku lake lakuti Elephant Memories, iye akulemba kuti: “Ndaona mikota yaikulu yolemekezeka ikutsogolera ndi kutetezera mabanja awo ndiponso ndaiona ikutaya kudzilemekeza kwawo ndi kuseŵera mothamangathamanga itapindilira michira yake kumsana kwake nkhope zake zikuoneka zachimwemwe ndithu.”

Daphne Sheldrick wa ku Kenya walera njovu zambiri zamasiye ndi kuzimasula kuzibwezera m’nkhalango. Pofunsidwa ndi magazini a Getaway, iye anati: “Ana a njovu onse amene ndimalandira amakhala ndi mikhalidwe yosiyana, monga momwe ana a anthu alili. . . . Iwo ali ndi mzimu wampikisano pang’ono, amachita nsanje ndipo pamene uwadzudzula amanyanyala. . . . Ena a iwo amapulupudza kapena kusamvera mwadala. Tiyenera kuwalanga, monga momwe mumalangira ana aumunthu.”

Kuwonjezera pa kukhala zosangulutsa, njovu zimachita mbali yothandiza m’chilengedwe. Chiŵerengero chake choyenera m’malo amodzi chimawonjezera mitundu yochuluka ya zomera. Buku lakuti Elephants, Economics and Ivory limandandalika ntchito zina zofunika kwambiri, zonga kuyambitsa madambo atsopano, kumwaza mbewu, ndi kuchepetsa “akambalame.” “Njovu,” akumaliza motero olembawo, “zili ndi mbali yofunika kwambiri pazomera, malo ndi zamoyo m’madambo ndi nkhalango za mu Afrika.”

Komabe, ngati pali njovu zambiri koposa zimawononga zomera. Apa mpamene zimakhala adani kwa anthu ena. Pachifukwa chimenechi, otetezera zinyama panthaŵi ndi nthaŵi amapha njovu m’malo ena aang’ono kuchepetsa chiŵerengero chake. Kumadera ena mu Afrika kumene njovu zili ndi malo otakata, kuphako sikumachitidwa. Zimenezi zili ndi mapindu ake. “M’nkhalango yosungira zinyama ya Amboseli ku Kenya,” akufotokoza motero magazini a New Scientist, “kumene kulibe kupha kochepetsa chiŵerengero, njovu zimayenda momasuka pakati pa anthu ndipo sizimawawopa.”

Asayansi akuyesayesa kupeza njira zina zochepetsera chiŵerengero cha njovu zomabadwa. Pakali pano, pamene munthu aphunzira zambiri ponena za njovu, mosakayikira adzapeza zifukwa zambiri zozionera monga mabwenzi.

[Mawu a Chithunzi patsamba 31]

Animals/Jim Harter/Dover Publications, Inc.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena