‘Mphunzitsi Wanga Anapempha Mabuku Ena 20’
DANIEL wazaka 17 anapatsidwa gawo pasukulu yake yasekondale ku Boston, Massachusetts, U.S.A., la kukonza nkhani yonena za chipembedzo cha ku Asia. Iye akuti: “Mphunzitsiyo anatilimbikitsa kupita kulaibulale kukafufuza. Ndinadziŵa kuti buku la Mankind’s Search for God, lofalitsidwa ndi Watch Tower Society, likathandiza kwambiri. Ndinapita nalo kusukulu ndi kulisonyeza kwa mphunzitsi. Iye anachita chidwi kwambiri ndi maumboni ake owona, kulondola kwake, ndi mpangidwe wake wa mafunso ndi mayankho kwakuti anaodetsa makope 20 a kalasi lonse. Iwo tsopano ndiasukulu ndipo amagwiritsiridwa ntchito ndi kalasi lililonse lotsatira. Chopereka cha $50 chinaperekedwa kuthandizira ntchito yathu yophunzitsa ya padziko lonse.”
Mankind’s Search for God ndibuku lamasamba 384 limene limasonyeza kufunafuna Mulungu kwa anthu kupyolera m’zipembedzo zazikulu za dziko. Latembenuzidwira m’zinenero 34, ndipo makope oposa mamiliyoni 15 agaŵiridwa. Ngati mungakonde kuŵerenga chofalitsidwa chosangalatsa chimenechi, chonde fikirani Mboni za Yehova pa Nyumba Yaufumu yapafupi nanu kapena lemberani kukeyala yapafupi ndi kwanu imene ili patsamba 5.