Msonkhano Wachigawo Wakuti “Mantha Aumulungu” Wayandikira
Masiku atatu opindulitsa a chilangizo cha Baibulo akukuyembekezerani pa Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wakuti “Mantha Aumulungu.” Mu Zambia mokha, misonkhano 49 yalinganizidwa kuchitika kumapeto kwa chaka chino. Chotero mudzakhoza kupezeka pa umene udzachitidwira pafupi ndi kumene mukukhala.
Msonkhanowo udzayamba ndi nyimbo zamalimba pa 09:20 pa Tsiku Loyamba, ndipo programu patsikulo idzatha pafupifupi 16:00 masana. Pa Tsiku Lachiŵiri, magawo adzayamba pa 09:00, ndipo adzatha pafupifupi 16:30. Programu pa Tsiku Lomaliza idzayamba pa 09:30 ndi kutha pafupifupi 16:15.
Pa Tsiku Loyamba mmaŵa nkhani yaikulu sidzangosonyeza chimene mantha aumulungu ali komanso idzafotokoza mapindu ake kwa awo amene amakulitsa mantha otero. Programu yonse ya msonkhano idzasonyeza mapindu ameneŵa.
M’nkhani yosiyirana ndi ya zitsanzo ya ola limodzi pa Tsiku Loyamba masana, mudzamva mmene mantha aumulungu angalimbitsire ukwati ndi moyo wabanja, ndiponso mmene angathandizire achichepere kukhalabe ochirimika pa kukhulupirika kwawo kwa Mulungu. Magawo pa Tsiku Loyamba adzatha ndi nkhani yogwira mtima yakuti “Chitonthozo kwa Ofedwa.” Mudzayamikira chidziŵitso chothandiza choperekedwa m’nkhani imeneyo kuchirikiza awo amene ataya okondedwa awo mu imfa.
Programu pa Tsiku Lachiŵiri idzasonyeza mmene mantha aumulungu angachirikizire kumamatira kwathu ku chitsogozo cha Yehova ponena za mpingo ndi utumiki wathu. Nkhani yakuti “Anthu Osasiyidwa ndi Yehova” idzafotokoza mmene lonjezo la Mulungu la kusasiya anthu ake liyenera kuwayambukirira m’dziko lamakono. Pambuyo pake masanawo, m’nkhani yakuti “Ŵerengani Mawu a Mulungu, Baibulo Loyera, Tsiku ndi Tsiku,” nthumwi zidzalandira malingaliro ogwira ntchito a kuŵerenga ndi kuphunzira Baibulo. Programu pa Tsiku Lachiŵiri idzatha ndi nkhani yochititsa chidwi ya mutu wakuti “Tsiku Lowopsa la Yehova Lili Pafupi.”
Mbali yaikulu paprogramu ya pa Tsiku Lomaliza ndi nkhani yakuti “Kudzakhala Kuuka kwa Olungama.” M’nkhani yotsatira yakuti, “Kupulumutsidwa Amoyo Kupyola Chisautso Chachikulu,” malongosoledwe adzaperekedwa ponena za lonjezo labwino koposa la Yesu lokhudza awo amene sadzafa konse.—Yohane 11:26.
Gawo lammaŵa pa Tsiku Lomaliza lidzamalizidwa ndi drama yosonkhezera maganizo yamphindi 40 ya mutu wakuti Zosankha Zimene Mukuyang’anizana Nazo. Omvetsera adzatengeredwa ku tsiku la Yoswa ndipo adzaona chosankha chake chotsimikiza cha kutumikira Yehova chikusonyezedwa. Ndiponso adzaona chiyeso cha moto m’masiku a Eliya, ndipo maphunziro amene adzathandiza nthumwizo kusonyeza mantha aumulungu lerolino adzaperekedwa ndi zochitika ziŵiri zimenezi.
Pa Tsiku Lomaliza masana mbali yaikulu ya msonkhano idzakhala nkhani yapoyera yakuti, “Chifukwa Chake Tiyenera Kuwopa Mulungu Woona Tsopano Lino.” Kunena zoona mudzapindula mwa kupezekapo masiku onse atatu! Mukuitanidwa ndi mtima wonse kudzapezekako. Kuti mupeze malo apafupi ndi kwanu, kafunseni ku Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova yakumaloko, kapena lemberani ofalitsa magazini ano.
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
T. Rosenthal/SUPERSTOCK