Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 5/8 tsamba 32
  • Msamariya Wachifundo Wamakono

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Msamariya Wachifundo Wamakono
  • Galamukani!—1994
Galamukani!—1994
g94 5/8 tsamba 32

Msamariya Wachifundo Wamakono

MKAZI wina wokwatiwa ku Canada anavulala pangozi ya galimoto. Msamariya wachifundo wina wamakono anamthandiza. (Luka 10:29-37) Atachita chidwi ndi kukoma mtima kwake, mkaziyo analembera The Georgetown Independent zotsatirazi:

‘Kwa Mkonzi:

‘Ndikulemba kalata ino kaamba ka zifukwa ziŵiri. Choyamba, ndikufuna kuthokoza munthu wina wokhala mu Georgetown amene anandithandiza mlungu wathawu nditalephera kuwongolera galimoto langa ndi kugwera m’ngalande.

‘A John Saunders anali kudutsa ndi galimoto lawo ndipo anaima. Iwo anayamba kundipatsa chithandizo cha mankhwala choyambirira ndipo anali otonthoza. Anakhala nane kufikira pamene oyendetsa ambulansi ndi galimoto ya polisi anawalandira ntchitoyo. Chitaganya chanu nchodalitsidwa pokhala ndi Msamariya Wachifundo wonga a Saunders amene amakhala nanu.

‘A Saunders anafika kudzaona ine ndi amuna anga kuchipatala, kungoti adzatsimikizire kuti ndinali bwino. Ndinadabwa pozindikira kuti a Saunders amagwira ntchito kumalikulu a Mboni za Yehova ku Georgetown. Nthaŵi zonse ndinkaganiza kuti anthu amenewo samagwiritsira ntchito mankhwala, ndipo panopo mmodzi wa iwo anali atagwiritsira ntchito maphunziro a chithandizo cha mankhwala choyambirira kwa ine. Zimenezi zikundifikitsa pa chifukwa chachiŵiri cholembera kalatayi.

‘Ndikufuna kupepesa kwa Mboni za Yehova zonse chifukwa cha chipongwe chimene ndazichitira pamene zafika pakhomo panga. Nthaŵi zonse ndakhala ndikukhulupirira kuti ndinu otengeka maganizo. A Saunders anasonyeza lingaliro loipa limeneli kukhala lolakwika. Nonsenu ndinu anthu olingalira zinthu mwanzeru amene mukuyesa kuchita zimene mukulingalira kuti nzabwino.

‘Ndikuthokozaninso kachiŵiri, a Saunders, ndipo mamatiranibe kuzikhulupiriro zanu. Mulungu akudalitseni.

‘ T.M., Toronto’

Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti ‘uyenera kukonda mnansi wako monga iwe mwini.’ (Luka 10:27) Ngati mukukhumba kuphunzira zambiri ponena za Mboni za Yehova kapena ngati mukufuna kukhala ndi phunziro la Baibulo lapanyumba laulere, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 33459, Lusaka 10101, kapena kukeyala yoyenera yopezeka patsamba 5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena