Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 7/8 tsamba 15-19
  • Nyumba Zachifumu Zonyezimira za Pansi pa Nthaka za Moscow

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nyumba Zachifumu Zonyezimira za Pansi pa Nthaka za Moscow
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Inakhalirako
  • Kupenda Mosamalitsa
  • Magetsi ndi Mpweya
  • Chitamando Kuchokera ku Mbali Zonse
  • Ulendo Wobwereza wa ku Russia
    Galamukani!—1995
  • Anthu a Yehova Awina Milandu Imene Yatenga Nthawi Yaitali
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Umodzi Umene Umadabwitsa Dziko
    Galamukani!—1994
  • St. Petersburg “Zenela” la Russia Loonerapo Ulaya
    Galamukani!—2003
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 7/8 tsamba 15-19

Nyumba Zachifumu Zonyezimira za Pansi pa Nthaka za Moscow

NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! MU RUSSIA

SIKUNALI kovuta kudziŵa kumene kunali njanji ya pansi panthaka, kapena Metro. Unyinji wosalekeza wa anthu unali kutsikira ku khomo lopita pansi panthaka. Pamwamba pa khomolo panali chilembo cha M, chikumaŵala m’maonekedwe ofiira monyezimira. Zitseko za khomolo zinanditsegukira. Mkatimo ndinayang’anizana ndi maonekedwe ochititsa chidwi a anthu akumatsika ndi kuzimiririka mofulumira ngati kuti akuloŵa m’phompho. Poyamba ndinazengereza. Ndiyeno, ndikumadzilimbikitsa mwamphamvu, ndinatsatira.

Kwa nthaŵi yoyamba m’moyo wanga, ndinali m’njanji ya pansi panthaka. Sinali njanji ya pansi panthaka wamba—Metro ya Moscow! Koma m’dziko limene munthu angayende m’mlengalenga, kutsegula atomu, ndipo ngakhale kuchita opaleshoni yocholoŵana ya ubongo, kodi chachilendo nchiyani ndi njanji ya pansi panthaka?

Choyamba, ndinauzidwa kuti mwinamwake Metro ya Moscow ili njanji ya pansi panthaka yokongola koposa m’dziko. Monga momwe mwambi wina wa ku Russia umanenera, “nkwabwino kwambiri kuona chinthu china kamodzi ndi maso ako koposa kumva za icho nthaŵi zana.” Pamene ndinafikapo pa msonkhano wamitundu wa Mboni za Yehova mu Moscow July wathayo, ndinali ndi chidwi chokwera Metro.

Mmene Inakhalirako

Mu 1902 wasayansi ndi injiniya wa ku Russia wotchedwa Bolinsky anapereka lingaliro la kumanga dongosolo loyendera lapamtunda limene likapita m’mphepete mwa khoma la Kremlin ndi kuzungulira pakati pa mzinda. Koma konsolo ya mzinda wa Moscow inakana mapulani opanga dongosololo panthaŵiyo. Zaka khumi pambuyo pake konsoloyo inayamba kulingalira mwamphamvu za lingalirolo—linali kudzakhala loyamba la mtunduwo m’Russia—koma kuulika kwa Nkhondo Yadziko I mu 1914 kunachedwetsa zochitika zowonjezereka. Lingalirolo linadzutsidwanso mu 1931. Pamenepo mpamene Central Committee ya Chipani cha Communist cha Soviet Union inalamula kuti njanji yoyamba ya pansi panthaka ya dzikolo inayenera kumangidwa m’Moscow. Motero Russia anakhala dziko la 11, ndipo Moscow anakhala mzinda wa 17, kuyamba ntchito yaikulu koposa yomanga yoteroyo.

Metropolitan Subway ya Moscow inatsegula njanji yake yoyamba, yokhala ndi njanji ya utali wa pafupifupi makilomita 11, pa 7 koloko mmaŵa pa May 15, 1935, zaka zitatu zokha pambuyo pa kuyambika kwa kumangako. Masitima anayi anali kupita ku masiteshoni 13, ndipo anali okhoza kunyamula okweramo pafupifupi 200,000 patsiku. Nzika za Moscow ndi alendo anachita chidwi. Zinali zatsopano kwambiri, zachilendo kwambiri! Madzulo anthu anadikirira pamzera kuti akhale pakati pa okweramo oyambirira. Chinali chinthu china chofunikira kuonedwa. Ndipo zidakali zotero.

Chiyambire 1935 dongosololo lakulitsidwa kufika pa njanji zisanu ndi zinayi zimene zimafola mtunda wa pafupifupi makilomita 200 ndi zimene zili ndi masiteshoni 149. Pafupifupi mitundu ina yonse ya zoyendera za anthu onse m’Moscow, kuphatikizapo bwalo la ndege ndi njira za m’madzi, nzogwirizana mwa njira ina ndi ulendo wa pa Metro. Kwenikweni, nzika za Moscow sizingalingalire za moyo popanda Metro. Zimenezo nzanzeru, popeza kuti tsiku lililonse imatenga avareji ya okweramo mamiliyoni asanu ndi anayi, pafupifupi kuwirikiza kaŵiri chiŵerengero cha anthu a ku Finland. Poyerekezera, njira za pansi panthaka za London ndi New York City pamodzi zimatenga pafupifupi theka lokha la chiŵerengerocho.

Kupenda Mosamalitsa

Kodi muli ndi chidwi chofuna kuona zimene zili pansi panthaka m’nyumba zosanja 20? Makwerero amagetsi akutipereka pansi mofulumira. Ali amodzi a makwerero amagetsi pafupifupi 500 m’dongosolo lonselo, amene ngati aikidwa molumikizidwa angafike mtunda woposa makilomita 50. Ndipo kuli kokondweretsa chotani nanga, kutsikira pansi pa madigiri 30 pa liŵiro la pafupifupi mita imodzi pa kamphindi—pafupifupi kuwirikiza kaŵiri liŵiro la makwerero amagetsi a m’maiko ena ambiri!

Taloŵa m’siteshoni ya Mayakovskaya. Kamangidwe kake kakutipangitsa kulingalira ngati kuti tili m’nyumba yachifumu osati siteshoni ya njanji ya pansi panthaka. Ndikukupeza kukhala kovuta kulingalira kuti tilidi pansi panthaka. Sindimaona kaŵirikaŵiri kamangidwe kokongola koteroko pamtunda, ndipo sikamaonedwa kwambiri pansi panthaka. Nzosadabwitsa kuti chionetsero cha mitundu yonse cha kamangidwe chimene chinachitika pakati pa 1937 ndi 1939 chinapereka mphotho ku masiteshoni asanu a Metro ya Moscow, kuphatikizapo inoyo. Ndithudi, si masiteshoni onse 149 amene ali ooneka monga achifumu ngati siteshoni ya Mayakovskaya; ambiri atsopano sali opambanitsa—komabe ndi okongolabe—iliyonse yapadera mu mtundu ndi kapangidwe.

Pafupifupi masiteshoni onse ali ndi kenakake konena ponena za mbiri ya Russia. Nsangalabwi, dongo lootcha, ndi granite zinatengedwa kuchokera ku malo 20 osiyanasiyana a Russia kuti zidzagwiritsiridwe ntchito kukongoletsera. Motero, chithunzithunzi chosonyeza chimati: “Dziko lonse linakhamukira kudzathandiza kumanga Metro ya Moscow.” Granite inagwiritsiridwa ntchito kwambiri kukongoletsera pansi chifukwa cha kulimba kwake. Imeneyi ndi mfundo yofunika polingalira za makamu a anthu amene amadzaza tsiku ndi tsiku m’masiteshoniwo.

Pamene tikusangalala ndi kukongola kwa nyumba yachifumu ya pansi panthaka imeneyi, tikuona masitima odutsana oyenda pa liŵiro lalikulu. Pafupifupi timphindi 90 kapena kuposapo pambuyo pa kunyamuka kwa ina pa siteshonipo, magetsi a yotsatira akuonekera kale kuti ikuyandikira. Kodi nthaŵi zonse masitima amayenda kwambiri chonchi? Amatero panthaŵi imene anthu ali ochuluka. Koma kaŵirikaŵiri amasiyana ndi pafupifupi mphindi zitatu kufika ku zisanu.

Sitinakhazikike pamipando yathu yawofuwofu pamene tikuona mmene sitimayo imawonjezerera mofulumira liŵiro. Ikuyenda mwaphokoso kudzera m’mphako ya mamita asanu ndi imodzi okha m’bwambi, nthaŵi zina pa liŵiro lofika ku makilomita 100 pa ola limodzi. Eya, munthu angayende mtunda wonse wa Metro pafupifupi m’maola asanu ndi limodzi! Nzika za Moscow zimakonda Metro osati kokha chifukwa chakuti ili njira yofulumira koposa yoyendera ulendo koma chifukwa chakuti n’njotsika mtengo ndiponso n’njabwino. July watha, mkati mwa msonkhano wamitundu yonse wa Mboni za Yehova, kukwera kupita kulikonse pa Metro kunali ma ruble khumi, amene panthaŵiyo anali olingana ndi penny imodzi ya ku U.S.

Kusiyana kwa nthaŵi za masitimawo nkochepa kwakuti mungadabwe kuti zimatheka bwanji kuti masitimawo adzithamanga pa liŵiro lalikulu chotero. Kalongosoledwe kake nkokhweka. Dongosolo la zolamulira liŵiro zogwira ntchito zokha linalinganizidwira kuletsa ngozi. Dongosolo limeneli limatsimikizira kuti mtunda wa pakati pa masitima sumachepa konse kuposa mtunda umene ukafunikira kuimitsa sitimayo pa liŵiro limenelo. M’mawu ena, sitima imene ikuyenda pa liŵiro la makilomita 90 pa ola limodzi imene ikuyandikira kwambiri sitima imene ili kutsogolo kuposa mtunda woyenerera kuimitsa imayamba kumanga yokha mabuleki. Kuwonjezerapo, injiniya wa m’sitima yapatsogoloyo amachenjezedwa ndi chizindikiro cha ngozi. Ndithudi, dongosolo limeneli lawonjezera kwakukulu chitetezo pa ulendo. Kodi chimenecho chingakhale chifukwa chake nzika za Moscow zoyenda pa Metro zimakhala zodekha ndi zomasuka eti? Ambiri a iwo amakhala mwabata akumaŵerenga, mwachionekere ali ndi chidaliro chakuti akafika motetezereka kumene akupita.

Magetsi ndi Mpweya

Mmamaŵa uliwonse, pamene mainjini amagetsi zikwi zambiri ayamba kulira ndi mazana zikwi za magetsi ayamba kuyaka, mamiliyoni a anthu amayamba kudzipapatiza kudutsa nyumba zachifumu zapansi panthaka zodzaza ndi anthu kumene ngolo za sitima zokwanira pafupifupi 3,200 zidzakhala zikusinthana kutsegula ndi kutseka zitseko zawo tsiku lonse. Zonsezi zimatheketsedwa ndi unyinji wochuluka koposa wa magetsi.

Ntchito imeneyi imachititsa kutentha kochuluka, kumene, mwapang’ono kumaloŵa m’dothi la pozungulirapo. Koma bwanji ponena za kutentha kotsala kumene kungatenthetse kwambiri mphakozo ndi masiteshoniwo? Eya, monga momwe kumayenerera nyumba zachifumu, siteshoni iliyonse ili ndi dongosolo la mpweya limene limakonzanso kotheratu mpweyawo kuwirikiza nthaŵi zinayi pa ola. Mpweya wabwino umakhalapo nthaŵi zonse, mosasamala kanthu kuti Metro njodzaza motani. Kwenikweni, dongosolo la mpweya la Metro ya Moscow limalingaliridwa ndi ambiri kukhala labwino kopambana m’dziko.

Komabe, m’nyengo yachisanu, kutentha kumeneku kumakhala kothandiza. Kupatulapo kokha nyumba ndi njira zokhala pamwamba panthaka, dongosolo lotenthetsera silimafunikira. Masitimawo, makamu a anthu, ndi dothi lenilenilo, pokhala zitasunga kutentha kokwanira mkati mwa nyengo ya ngululu ndi dzinja, mooloŵa manja zimapereka kutentha kokwanira kufunditsa bwino nyumba zachifumu zapansi panthakazo.

Chitamando Kuchokera ku Mbali Zonse

Monga momwe kungayembekezeredwe, kabuku kosonyeza alendo kokhala ndi zithunzithunzi ka Metro kamatamanda kwambiri kuti: “Metro ya Moscow moyenerera imaonedwa kukhala yokongola koposa m’dziko, imene masiteshoni ake achifumu okhala ndi choloŵanecholoŵane wa njanji, mawaya, mipope ndi nsambo amaimiradi msakanizo wabwino koposa wa kuyesayesa kwa amisiri ndi luso la uinjiniya. Koposa kukhala chabe masiteshoni, ameneŵa ali kwenikweni maluso apadera osatsanzirika a zomangamanga a ulemerero ndi kukongola okometseredwa bwino ndi nsangalabwi, granite, chitsulo ndi matailosi, magetsi olinganizidwa mumpangidwe wamakono, kusemasema, kuwomba, kuumba, kumalemberera, galasi la mitundumitundu, ndi zokhomerera zaluso. Akatswiri enieni omanga ndi a zopangapanga a dzikolo,” kuphatikizapo osemasema, “anathandizira kulinganiza ndi kukongoletsa.”

Tsopano, pambuyo popita ku Moscow ndi kudzionera ndekha Metro, ndingavomereze. Nthumwi zinzanga ku msonkhanowo zinachitanso chidwi. Mjeremani wina anandiuza kuti: “Ndinaona ngati kuti ndinaloŵa m’nyumba ya konsati yokhala ndi magetsi anthambi. Ndinakondweretsedwa kwambiri.” Mlendo wochokera ku United States anachita chidwi kwambiri ndi kusunga nthaŵi, udongo, ndi kudalirika kwa Metro. Ndipo nthumwi ya ku msonkhano yochokera ku Siberia wakutaliyo inadabwa ndi ukulu ndi mlingo wa nyumba za pansi panthakazo.

Mukadzapita ku Moscow, ndingakonde kukufulumizani kuchezera nyumba zachifumu zonyezimira za pansi panthaka zimenezi. Kumbukirani: “Nkwabwino kwambiri kuona chinthu china kamodzi ndi maso ako koposa kumva za icho nthaŵi zana.”

[Mawu a Chithunzi patsamba 15]

Sovfoto/Eastfoto

[Chithunzi pamasamba 16, 17]

Masiteshoni oŵerengeka okongola a pansi pa nthaka a Moscow

[Mawu a Chithunzi]

Magwero a zithunzi (kuyambira pamwamba kulamanzere kupita kulamanja): Laski/Sipa Press; Sovfoto/Eastfoto; Sovfoto/Eastfoto; Laski/Sipa Press; Laski/Sipa Press; Sovfoto/Eastfoto

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena