“Ndili Wokondweretsedwa ndi Kuphunzira Zowonjezereka”
MWAMUNA wina wa ku Colorado, U.S.A., analemba zapamwambazo December watha m’kalata yopita kwa afalitsi a magazini ano. Iye analongosola kuti:
“Ngakhale kuti simungandilingalire kukhala munthu wachipembedzo mogwirizana ndi miyezo ya anthu ochuluka, nthaŵi zonse ndakhulupirira kuti payenera kukhala zowonjezereka ku moyo kuposa zimene timaona ndi kumva m’kukhalapo kwathu kwa tsiku ndi tsiku. Nthaŵi zonse ndakhala ndi kudzipereka kwauzimu, ngakhale kuti sindinachite zimenezo ku chipembedzo chinachake.
“Komabe, posachedwapa ndadzipeza ndili m’mikhalidwe ina yovutitsa maganizo kwambiri ndi kudzipeza ndikusoŵa nyonga ya mkati yolakira mikhalidweyo. Mavuto a kunyumba ndi kuntchito awonjezera ukulu wa nkhaŵa yanga kufika pa mlingo umene sindinaonepo ndi kale lonse. . . .
“Modabwitsa kwenikweni, pamene ndinali pachimake pa kugwiritsidwa mwala kwanga, ndinapeza mwangozi chimodzi cha zofalitsidwa zanu pa masitolo. Malingaliro anu onena za Atate Woyera ali otsitsimula, ndipo ndili wokondweretsedwa ndi kuphunzira zowonjezereka, koma sindili wotsimikizira kuti nditembenukire kuti.
“Ndingayamikire kwambiri chitsogozo chilichonse chimene mungandipatse kuti ndiphunzire zowonjezereka ponena za Mboni za Yehova ndi zikhulupiriro zanu. Monga ndanena, ndinaziona kukhala zodabwitsa kupeza mwangozi chimodzi cha zofalitsidwa zanu pachimake pa kugwiritsidwa mwala kwanga—mwina chingakhale chizindikiro cha chitsogozo chaumulungu.”
Mwamunayu anatumiziridwa kope la buku limene limapereka zikhulupiriro zozikidwa pa Baibulo za Mboni za Yehova, la mutu wakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. Ngati mungakonde kulandira kope la chofalitsa chimenechi cha masamba 256 cha chikuto cholimba kapena kukhala ndi phunziro la Baibulo lapanyumba laulere, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 33459, Lusaka 10101, kapena ku keyala yoyenerera yondandalikidwa patsamba 5.