Mankhwala a Vuto la Kusankhana Mafuko
Posachedwapa mwamuna wina wa ku Oklahoma, U.S.A., analandira kope la magazini a Galamukani! limene linali ndi nkhani yakuti “Kodi Mafuko Onse Adzagwirizana Konse?” Poyamba kulemba kalata yakeyo ndi mawu akuti “Afalitsi a Watchtower Okondedwa,” munthuyo analemba kuti:
“Ndinali ndi mwaŵi wabwino wa kuŵerenga kope lanu la Galamukani! la September 8, 1993, posachedwapa, losimba za vuto la maunansi a mafuko. Ndinadabwa, ndipo ndinachita chidwi, ndi kufotokoza kwanu kosakondera ndi kuzindikira kwanzeru pa vuto locholoŵana limeneli.
“Ndamaliza kosi ya mbiri ya United States pakoleji posachedwapa. Koma m’masamba 9 okha a magazini anu munapereka mbiri yaifupi, mafotokozedwe, NDI MANKHWALA a vuto lobisika limeneli amene akupambana a maphunziro onse a m’mabuku a kukoleji a miyezi isanu ndi umodzi. Nkhani zake zinali zofotokozedwa mosakondera kwakuti nkovuta kudziŵa fuko la olembawo.
“Pamene dziko likhala logaŵanikagaŵanika mowonjezereka chifukwa cha kusankhana mafuko, munthu aliyense afunikira kuŵerenga chidziŵitso cha mtundu umenewu chochuluka chofalitsidwa monga momwe mungathere. Ndikukuthokozani chifukwa cha kukhala kwanu olimba mtima kufalitsa choonadi ndi nzeru yozoloŵereka.”
Ngati mungakonde kuti kope la Galamukani! lizitumizidwa kwanu, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 33459, Lusaka, kapena ku keyala yoyenerera yondandalikidwa patsamba 5.