Deti Limene Simuyenera Kuiŵala
Madzulowo Yesu asanamwalire, anagaŵana mtanda wa mkate wopanda chotupitsa ndi chikho cha vinyo ndi atumwi ake nati: “Chitani ichi chikumbukiro changa.”—Luka 22:19.
Chaka chino chochitikacho chidzakhalako pa Lachisanu April 14 dzuŵa litaloŵa. Chifukwa cha kumvera lamulo la Yesu, mamiliyoni a Mboni za Yehova ndi anthu okondwerera padziko lonse adzasonkhana usiku wapadera umenewu kuchitanso Chikumbutso chimenechi m’njira imene Yesu analangiza. Mukuitanidwa mwachikondi kudzasonkhana nafe. Chonde funsani Mboni za Yehova za kwanuko ponena za nthaŵi yeniyeni ndi malo osonkhanira.