Chithandizo cha Achichepere Opsinjika Mtima
Pamene mtsikana wina pasukulu ya ku New Jersey, U.S.A., anavutika maganizo ndi kuthaŵa m’kalasi, mnzake wam’kalasi anamlondola kuchipinda cha atsikana. “Pamene ndinampeza,” mnzake wam’kalasiyo anatero, “anali kulira nandiuza za ena a mavuto a banja lake. Makolo ake anali kusudzulana, ndipo anati kunali kovuta kusumika maganizo ake pa maphunziro. Anandiuza kuti anafuna kuthaŵa pa nyumba.”
Mnzakeyo anauza mtsikana wovutika maganizoyo kuti angakonde kumbweretsera buku lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza. Tsiku lotsatira analibweretsa, ndi kusonyeza bwenzi lake mitu yonga ngati “Kodi Nchifukwa Ninji Ndiyenera ‘Kulemekeza Atate Ŵanga ndi Amayi Ŵanga’?,” “Kodi Nchifukwa Ninji Amayi ndi Atate Analekana?,” “Kodi Ndingalake Motani Chitsenderezo cha Ausinkhu Wanga?,” ndi “Kodi Ndiyenera Kuchoka pa Nyumba?”
“Pamene ndinampatsa bukulo,” anatero mnzakeyo, “atsikana ena aŵiri analiona ndipo analikhumbira. Anafunsa ngati iwonso angakhale ndi makope awo. Motero aliyense ndinampatsa kope lake. Achichepere ena m’kalasi langa anaona mmodzi wa atsikanawo akuyang’ana m’masamba a bukulo, ndipo onse anafuna kuliona. Bukulo potsirizira pake linapatsidwa m’manja mwa aliyense m’kalasilo kuliona ataloledwa ndi m’phunzitsi.”
Ngati mungakonde kukhala ndi kope la Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza kapena mungakonde kukhala ndi phunziro la Baibulo lapanyumba laulere, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 33459, Lusaka 10101, kapena ku keyala yoyenera yondandalitsidwa patsamba 5.