Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 1/8 tsamba 18
  • Mapemphero a Mtendere Pakati pa Zikumbukiro za Nkhondo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mapemphero a Mtendere Pakati pa Zikumbukiro za Nkhondo
  • Galamukani!—1996
  • Nkhani Yofanana
  • Tchalitchi cha Katolika mu Afirika
    Galamukani!—1995
  • ‘Manja Anu Adzaza ndi Mwazi’
    Galamukani!—1987
  • Chipembedzo Chichirikiza Mbali Ina
    Galamukani!—1994
  • Ulendo wa Papa ku UN Kodi Unakwaniritsanji?
    Galamukani!—1996
Onani Zambiri
Galamukani!—1996
g96 1/8 tsamba 18

Mapemphero a Mtendere Pakati pa Zikumbukiro za Nkhondo

MU November 1994, Papa John Paulo II anaitanitsa msonkhano wa zipembedzo zosiyanasiyana mu Vatican. Chochitika chachikulu pamenepo chinali mapemphero a mtendere wapadziko lonse. “Kaya kale panali mikangano kapena pali mikangano iliyonse tsopano,” anatero papayo m’mawu ake otsegulira msonkhano, “ndi ntchito yathu ndi thayo lathu kudziŵikitsa bwinopo unansi umene uli pakati pa chipembedzo ndi mtendere.”

Mosiyana ndi zimenezo, zipembedzo za dzikoli zili ndi mbiri yoipa pankhaniyi. William Vendley, mlembi wamkulu wa msonkhanowo, anavomereza kuti “zipembedzo zili zoloŵetsedwamo kwambiri m’mikangano ya m’mbali zambiri zadziko.” Talingalirani za kupulula anthu ku Rwanda, dziko la Aroma Katolika ochuluka koposa.

M’May 1994, Papa John Paul II anavomereza kuti nkhondo ya ku Rwanda inali “kupulula mtundu wonse kwenikweni kumene, mwatsoka, ngakhale Akatolika ali nako mlandu.” Kodi kutengamo mbali kwa Akatolika kwayambukira chikhulupiriro cha anthu pa tchalitchicho? “Kupulula anthuko kwasokoneza chikhulupiriro cha ambiri,” anatero André Bouillot, m’Jesuit wa ku Belgium. Ndipo anatero ndi chifukwa chabwino.

Malinga ndi lipoti la Reuters lofalitsidwa mu Herald ya ku Miami, “ansembe, abusa ndi avirigo ali pakati pa andende 40,000 a mtundu wachihutu amene akuyembekezera kuimbidwa mlandu wa kupulula mtundu wonse wa anthu.” The New York Times inanena kuti: “Arwanda ambiri akunena kuti mabishopu awo ndi maakibishopu awo sanatsutse kupha kosakaza kumeneko mwamsanga kapena mwamphamvu ndi kuti anali mabwenzi kwambiri ndi Boma la Habyarimana, limene linathandizira kuphunzitsa magulu akupha. Wansembe mmodzi wamangidwa ndi Boma latsopano la Atutsi ambiri pa mlandu wa kugwirizana ndi kupha kosakazako.” Mosadabwitsa, “Boma latsopano,” ikuwonjezera motero Times, “likunena kuti silikufuna kuti Tchalitchi cha Katolika chikhale champhamvu monga mmene chinalili poyamba, ndipo asilikali asautsa ansembe ngakhale kuwaopseza kuti adzamanga aliyense wa iwo amene amalankhulalankhula ndi amene ali wodziimira.”

Kodi ndi motani mmene Yehova Mulungu amaonera mapemphero amtendere amene amaperekedwa ndi anthu achipembedzo okhala ndi liwongo la mwazi? Yesaya 1:15 akuyankha kuti: “Pamene mutambasula manja anu, ndidzakubisirani inu maso anga; inde pochulukitsa mapemphero anu ine sindidzamva; manja anu adzala mwazi.”

Izi zidakali choncho, atumiki oona a Yehova akupitirizabe kusakhala “a dziko lapansi” ndi mikangano yake yonse. Mkati mwa kupha kosakaza ku Rwanda, Mboni za Yehova za mumtundu uliwonse zinabisa Mboni zokhala pangozi za mtundu wina m’nyumba zawo, motero zikumazitetezera mwakuika moyo wa iwo eni pachiswe. “Khamu lalikulu” la Mboni, lapadziko lonse lopangidwa ndi mitundu yonse, limapempherera ndi kuchirikiza Ufumu wa Mulungu monga chiyembekezo chokha cha mtendere weniweni ndi chisungiko.—Yohane 17:14; Chivumbulutso 7:9; Mateyu 6:9, 10; 24:14.

[Mawu a Chithunzi patsamba 18]

Luc Delahaye/Sipa Press

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena