Dzitetezereni ku Mphezi!
YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU SWEDEN
MPHEZI wamba ingakhale ndi mphamvu ya magetsi yokwana ma volt mamiliyoni makumi ambiri ndi ma ampere zikwi makumi. Titalinganiza, magetsi odziŵika a m’nyumba kaŵirikaŵiri amaikidwa pa ma ampere 15.a Kodi mungachitenji kuti muchepetse ngozi ya kukanthidwa ndi mphezi? Taonani njira zotsatirapozi.
• Ngati kuli kotheka, loŵani m’nyumba. Ngakhale galimoto lingakhale chitetezo chabwino. Bwanji ponena za kukhala m’nyumba yosanja? Nyumba yosanja yokhala ndi zitsulo zogwira mphezi ingakhale malo abwino. Mwachitsanzo, Empire State Building mu New York City imapulumuka kukanthidwa ndi mphezi pafupifupi nthaŵi 25 chaka chilichonse. Komabe, kuli bwino kwambiri kupeŵa nyumba zimene zilibe zitsulo zozigwirizanitsa ndi nthaka zimene zili ndi denga lachitsulo ndi malo okhala pafupi ndi mlongoti wogwira ndi kuulutsa mawu kapena linga lachitsulo.
• Chokani pamalo opanda kanthu, monga nyanja, minda, ndi moseŵerera golf. Nayonso mitengo yokhala payokha, ndipo imene ili yaitali ingakhale yangozi. Ngati muli pamalo okhala ndi mitengo yambiri, bisalani pafupi ndi yaifupi kwambiri. Ngati mkuntho mwangozi uli pafupi ndipo simungachoke pamalo opanda kanthuwo, utamani pansi ndipo fungatirani maondo anu. Musagone pansi, pakuti nkofunika kwambiri kuti musapereke malo aakulu pamene mphezi ingakanthe.
• Ngakhale pamene muli m’nyumba, muyenera kukhala osamala. Zotsatirapozi ndi njira zingapo: Yesani kupeŵa kukhudza zinthu zimene zingatenge magetsi, monga mokhala moto ndi mipope yachitsulo. Nkwanzeru kuchoka mosambira, ndipo yesani kusagwiritsira ntchito foni. Chotsani mapulagi a makompyuta, mawailesi a kanema, ndi ziŵiya zina, popeza zingawonongeke ngati nyumba yakanthidwa ndi mphezi.
• Ngati wina wakanthidwa ndi mphezi, nkofunika kwambiri kumtsitsimutsa mwa kumuuzira mpweya mkamwa (CPR [cardiopulmonary resuscitation]) pomwepo. Profesa Victor Scuka, amene amagwira ntchito mu Dipatimenti Yofufuza za Magetsi Amphamvu Kwambiri pa University of Uppsala, Sweden, akunena kuti nthaŵi zambiri okanthidwa ndi mphezi anayambanso kupuma ndi CPR, ngakhale pamene anaoneka monga afa. “Koma kuchizako,” akuchenjeza motero, “kuyenera kuchitidwa pomwepo kuti ubongo usawonongeke.”
Ngati mwapezeka mumkuntho wa mphezi, londolani njira zimene zangotchulidwazo. Motero sikudzakhala kwapafupi kwa inu kukanthidwa ndi chinthu chochititsa mantha chimenechi.
[Mawu a M’munsi]
a Ampere ndi mlingo wopimira kayendedwe ka magetsi, chiŵerengero cha magetsi amene akugwiritsidwa ntchito. Ma volt amasonyeza mphamvu ya magetsiwo. Onani Galamukani! wachingelezi wa February 22, 1985, masamba 26-7.