“Iwo Akhala Abwino Kwambiri!”
“Nthaŵi zonse ndakhala ndikusangalala kuŵerenga Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, koma m’zaka zino iwo akhala abwino kwambiri kwakuti sindingapeze mawu owafotokozera. Ndikufuna kuyamikira chidziŵitso chimene chili m’kope la Galamukani! la November 8, 1994, pansi pa mitu yakuti “Sarajevo—Kuyambira 1914 Kufikira 1994” ndi “Chipembedzo Chichirikiza Mbali Ina.” Nkhondo yachiŵeniŵeni ya pakati pa Bosnia, Serbia, ndi Croatia ili chochitika chocholoŵana ndi chomvetsa chisoni koma chimene ndimalingalirapo kwambiri monga wa ku Croatia. Ndinayamikira makamaka mmene munafotokozera mbiri ya mkanganowo ndi mizu yake yakuya yakale mu 1054. Chimenechi chinaonetsa poyera mbali ya chipembedzo ndi zoyesayesa zake zosalekeza zimene zachititsa mipatuko yambiri ndi udani pakati pa mafuko ameneŵa. Mwatsoka, dziko lerolino limangoona kuipa mwa anthuwa amene mwachibadwa ali abwino. Ndikukuyamikani kachiŵirinso kaamba ka kuchititsa mkhalidwe wosamvetsetseka kumvetsetseka. [Yosainidwa] M.K.”
Galamukani! wakhala ndi mbiri ya kufufuza kosamala ndi kulemba kopanda tsankhu. Koma alinso magazini amene amapereka chiyembekezo cha mtsogolo mwamtendere chozikidwa pa lonjezo la Mulungu la kukhazika dziko lapansi pansi pa ulamuliro wa Ufumu wake.
Ngati mungafune kuŵerenga magazini ameneŵa nthaŵi zonse, chonde lankhulani kwa Mboni za Yehova kwanuko, kapena lemberani ku keyala yoyenera yondandalikidwa patsamba 5 ya kope lino.
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
Zithunzithunzi za Culver