Musawawanye, Ndipo Simudzasoŵa
M’CHITAGANYA chathu chamakono cha ogula zinthu, kutaya zinyalala wamba ndi zinyalala zowopsa kosachititsa ngozi kwakhala kovuta kwambiri. Mosiyana ndi zimenezo, chilengedwe cha Mulungu chili chodabwitsa pa kusinira ndi kukonzanso zinthu zakale kuti zigwiritsiridwe ntchito. Mwachitsanzo, talingalirani za chisa cha njuchi. Phula, lomangira chisa, ndi chinthu chamtengo wapatali—njuchi yopanga uchi imafunikira magalamu 16 a uchi ndi unyinji wosadziŵika wa poleni kuti ipange galamu imodzi yokha ya phula. Kodi ndi motani mmene njuchi zimagwiritsirira ntchito phula lake? “Makoma atatu aphula a zipinda zachisa amakumana pamodzi pamadigiri 120, akumapanga zipinda zambiri zofanana za mbali zisanu ndi imodzi,” likufotokoza motero buku lakuti By Nature’s Design. “Mapangidwe ameneŵa amatheketsa njuchi kuchepetsa unyinji wa phula umene zimagwiritsira ntchito, pamene zikupanga malo olimba osungiramo uchi.” Chotero chinthu chomangidwa mwaluntha chimasanganiza kukongola kwa mpangidwe ndi kusinira pa ntchito yake, ndipo chikhoza kugwiritsiridwanso ntchito!
Ngati mumasangalala kuŵerenga nkhani za sayansi ndi zinthu zodabwitsa zachilengedwe ndipo mungakonde kumalandira Galamukani! nthaŵi zonse, onanani ndi Mboni za Yehova kwanuko kapena lemberani ku keyala yapafupi kwambiri yondandalitsidwa patsamba 5.