Tsamba 2
Ufulu wa Kulankhula—Kodi Ukugwiritsiridwa Ntchito Molakwa? 3-11
Malamulo apangidwa, nkhondo zamenyedwa, ndipo anthu ambiri afa mu nkhondo ya kukhazikitsa ufulu wa kulankhula. Tsopano anthu a malingaliro atsopano akulirira mwamphamvu kuchepetsedwa kwa ziletso zake.
Chifukwa Chimene Anasinthira Zinthu Zake Zoyamba 15
Ŵerengani nkhani yokondweretsa ya amene kale anali woyang’anira malo a nyama ku Minsmere, malo a mahekitala 800 ku England. Anasiya ntchito yakeyo kukaloŵa ina. Chifukwa ninji?
Kodi Nchifukwa Ninji Achichepere Ena Amangosangalala Mmene Amafunira? 27
“Timangofuna kusangalala, koma nzovuta kwambiri,” anadandaula motero Jason wazaka 15.