Tsamba 2
Kodi Boma lingathetse Upandu? 3-11
Kodi inuyo kapena wokondedwa wanu munakumanapo ndi upandu? Ngakhale kuti ngati simunatero, mudzakondwabe kudziŵa kuti boma lidzathetsa upandu posachedwapa. Koma motani? Ndipo kodi ndi boma liti?
Kodi Tili ndi Mlandu pa Zochita Zathu? 17-24
Lerolino pali chizoloŵezi cha kulungamitsa khalidwe losavomerezeka ndi mawu akuti, “Si mlandu wanga!” Palinso ambiri amene amalimbikira kunena kuti majini athu amatichititsa kukhala ndi chikhoterero cha makhalidwe opulupudza ndipo motero timangochita zimene zimadza mwachibadwa.
[Mawu a Chithunzi patsamba 2]
Chikuto ndi nyumba ya patsamba 2: U.S. National Archives photo