Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 11/8 tsamba 32
  • “Kufunafuna Waluso Wamkulu Koposa”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Kufunafuna Waluso Wamkulu Koposa”
  • Galamukani!—1996
Galamukani!—1996
g96 11/8 tsamba 32

“Kufunafuna Waluso Wamkulu Koposa”

Umenewo unali mutu wa nkhani wa Galamukani! wa November 8, 1995 m’Chingelezi. (M’Chicheŵa onani magazini amodzimodziwo, masamba 19-28.) Nkhaniyo inathokozedwa ndi oŵerenga ambiri kuzungulira dziko lonse.

Amang analemba kuchokera ku Douala, Cameroon, kuti: “Nkhanizo zinandikhudza kwambiri chifukwa ndimakonda zopangapanga, makamaka kujambula. Tsopano ndazindikira kuti kuli Mmisiri wokulirapo kuposa Van Gogh, Rembrandt, Da Vinci, ndi ena—ndipo ameneyo ndiye Yehova Mulungu mwiniyo.”

Kuchokera ku St. Barthélemy, mu French West Indies, Frederick anati: “Ndinaiŵerenga kanayi konse, ndipo nthaŵi iliyonse ndinali wodzala ndi chiyamiko kaamba ka zinthu zokongola zomwe Mlengi wathu anatipatsa.”

Assunta analemba kuchokera ku Italy: “Inadzutsa mwa ine chikhumbo cha kujambula. Inazamitsa chimwemwe changa kaamba ka dziko latsopano la Mulungu.” Ndipo Irena wa ku Czech Republic, anati: “Pamene timamka kukacheza ku myuziyamu, timalipira kuti tione maluso a zopangapanga, pamene Mlengi wa kukongola konse kwa chilengedwe amatipatsa kwaulere, tsiku ndi tsiku.” Aline analemba kuchokera ku Brazil: “Ngakhale kuti kaŵirikaŵiri timakhala ndi nkhani zimene zimatithandiza kumvetsetsa umunthu wa Yehova, izizo zinandilasa mtima. Zinapereka tsatanetsatane wochuluka ponena za chilengedwe chimene chimakulitsa chiyamikiro chathu cha chikondi cha Yehova.”

Kuchokera ku Wisconsin wozizira mu U.S.A., Anne analemba kuti: “Inandithandiza zedi kuyamikira kukongola kwa chilengedwe. Nthaŵi zina m’chisanu nkovuta kukupeza. Tsiku lomwelo nditangoŵerenga nkhaniyo, ndinatuluka panja nkukaona chisanu pa nthambi, tsamba lokutidwa ndi chipale chofeŵa, mapazi a ziŵeto pa chipale chofeŵa. Ndikuthokoza kachiŵirinso kaamba ka chikumbutso cha mmene tingathere kuyamikira ‘Mmisiri Wamkuluyo.’”

Ngati mungakonde kulandira magazini ameneŵa nthaŵi zonse, chonde fikirani Mboni za Yehova za pafupi ndi kwanuko kapena lemberani ku keyala yapafupi yondandalikidwa patsamba 5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena